Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 11/15 tsamba 22-23
  • ‘Pemphereranani’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Pemphereranani’
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nchifukwa Ninji Tiyenera Kupemphererana?
  • Kupempherera Chiyani?
  • Mikhalidwe Yachikristu Imakulitsidwa
  • Pitirizanibe Kupemphererana
  • Tili Ndi Mwayi Wopemphera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kuyandikira kwa Mulungu m’Pemphero
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kuti Mulungu Akhale Mnzanu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Mmene Mungapezere Chithandizo Kupyolera mwa Pemphero
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 11/15 tsamba 22-23

‘Pemphereranani’

YEHOVA ali “Wakumva pemphero.” (Salmo 65:2) Iye nthaŵi zonse amamva mapemphero a odzipereka kwa iye ndi mtima wonse, ndipo tingakhale otsimikiza kuti iye amamvetsera pamene amapemphererana.

Koma kodi nchifukwa ninji tiyenera kupemphererana? Kodi mapempherowo ayenera kuperekedwa ponena za chiyani? Ndipo kodi ndi mikhalidwe yaumulungu yotani imene imakulitsidwa pamene tipemphererana?

Kodi Nchifukwa Ninji Tiyenera Kupemphererana?

Malemba amalimbikitsa anthu a Yehova kumapemphererana. Mapemphero kaamba ka ena anali pakati pa zopempha za mtumwi Paulo kwa Mulungu. (Akolose 1:3; 2 Atesalonika 1:11) Ndiponso, wophunzira Yakobo analemba kuti: ‘Mupempherere wina kwa mnzake.’​—Yakobo 5:16.

Mapemphero kaamba ka atumiki ena a Mulungu amagwira ntchito. Izi zikusonyezedwa pa Yakobo 5:13-18, pamene Mkristu wodwala mwauzimu akulimbikitsidwa kulola akulu amumpingo kuti “apempherere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m’dzina la [Yehova, NW].” Kumvetsera mapemphero awo kungalimbitse munthu wopsinjikayo ndikumkhutiritsa kuti Mulungu adzayankhanso mapemphero ake. (Salmo 23:5; 34:18) Pambali popemphera ndi munthuyo, akulu amayesayesa kubwezeretsa thanzi lake lauzimu mwakulongosola malingaliro Amalemba amene ali ngati mafuta otonthoza.

Yakobo akuwonjezera kuti: ‘Pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Yehova adzamuukitsa.’ Inde, munthu wodwala mwauzimu mwachiwonekere angathandizidwe ndi ‘pemphero la chikhulupiriro’ la akulu. Ndiponso, Mulungu “adzamuukitsa” ku thanzi lauzimu ngati ali wofunitsitsa kuthandizidwa ndi Malemba. Koma bwanji ngati kudwala kwauzimuko kunachititsidwa ndi tchimo lalikulu? Eya, ngati munthuyo ali wolapa, Yehova adzamkhululukira.

‘Chifukwa chake,’ akutero Yakobo, ‘muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m’machitidwe ake. Eliya . . . anapemphera chipempherere kuti isavumbe mvula; ndipo siinagwa mvula pa dziko zaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi. Ndipo anapempheranso; ndipo m’mwamba munatsika mvula, ndi dziko lidabala zipatso zake.’ (1 Mafumu 17:1-7; 18:1, 42-45) Pemphero la munthu wolungama limakhala ndi mphamvu yogwirizana ndi chifuno cha Mulungu.​—1 Yohane 5:14, 15.

Kupempherera Chiyani?

Nkhani iriyonse tingaiyike m’mapemphero athu kaamba ka wokhulupirira mnzathu. Mwachitsanzo, Paulo anapempha ena kumpempherera iye kuti akhale ndi luntha lakulankhula mbiri yabwino. (Aefeso 6:17-20) Bwanji ngati timadziŵa kuti wina akuyesedwa? Tingapemphere kuti ‘asachite cholakwika’ ndikuti Mulungu asamsiye ku kuyesedwa koma kuti ampulumutse kwa woipayo, Satana Mdyerekezi. (2 Akorinto 13:7; Mateyu 6:13) Ndipo ngati wina akudwala mwakuthupi, tingapemphe Yehova kumpatsa kulimba kofunikira kuti apirire matenda ŵake.​—Salmo 41:1-3.

Nthaŵi zonse kuli koyenera kumapempherera alambiri anzathu a Yehova omazunzidwa. Paulo ndi anzake anavutika ndi chizunzo, ndipo anauza Akristu a ku Korinto kuti: ‘Pothandizana inunso ndi pemphero lanu la kwa ife; kuti pa mphatso ya kwa ife yodzera kwa anthu ambiri, payamikike ndi anthu ambiri chifukwa cha ife.’ (2 Akorinto 1:8-11; 11:23-27) Ngakhale ngati tiri m’ndende, tingapempherere abale ena ozunzidwa, tikumakumbukira nthaŵi zonse kuti Yehova amamvera “pemphero la olungama.”​—Miyambo 15:29.

Tiyenera kupempherera makamaka abale athu amene akusenza mathayo okulirapo mkati mwa gulu la Yehova. Ichi chimaphatikizapo awo amene amatsogolera gulu ndikukonza chakudya chauzimu choperekedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Mwachitsanzo, ziŵalo za Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova zimafunikira mapemphero athu, ndipo tingapemphere kuti Mulungu awapatse “mzimu wa nzeru.”​—Aefeso 1:16, 17.

Mikhalidwe Yachikristu Imakulitsidwa

Mwakupempherera okhulupirira anzathu, timadzisonyeza kukhala odera nkhaŵa, opanda dyera, ndi achikondi. Kudera nkhaŵa kopanda dyera, kwachikondi kaamba ka abale ndi alongo athu auzimu kumagwirizana ndi mfundo ya Paulo yakuti chikondi ‘sichitsata za mwini yekha.’ (1 Akorinto 13:4, 5) Kupempherera ena kuli njira imodzi ya ‘kusapenyerera zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.’ (Afilipi 2:4) Pamene tisonyeza nkhaŵa ya mkhalidwe wabwino wauzimu wa abale athu m’pemphero, timapezanso kuti ifeyo timayandikira kwa iwo m’chikondi chaubale chimene chimazindikiritsa ophunzira a Yesu.​—Yohane 13:34, 35.

Mkhalidwe wochitirana chifundo umakulitsidwa kulinga kwa amene timawapempherera. (1 Petro 3:8) Timawachitira chisoni, kumagaŵana m’zikondwerero zawo ndi zipsinjo. M’thupi lamunthu, ngati dzanja limodzi lavulazika, linalo limalisamalira ndikuyesayesa kuchepetsa kuvutitsa kwa chirondacho. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 12:12, 26.) Mofananamo, kupempherera abale ndi alongo ovutika kumakulitsa chifundo chathu kaamba ka iwo ndikutithandiza kuwakumbukira. Kuli kutaikiridwa kwathu ngati tinyalanyaza Akristu anzathu okhulupirika m’mapemphero athu, popeza kuti Mulungu ndi Kristu samawasiya iwo.​—1 Petro 5:6, 7.

Mikhalidwe yaumulungu yosiyanasiyana imakulitsidwa pamene timapempherera ena. Timakhala omvetsetsa ndi oleza mtima mowonjezereka kulinga kwa iwo. Kukwiyitsidwa kothekera kumazulidwa, kupereka mpata kaamba ka malingaliro omangirira amene amatikhalitsa achikondi ndi osangalala. Kupempherera ena kumachirikizanso mtendere ndi chigwirizano pakati pa anthu a Yehova.​—2 Akorinto 9:13, 14.

Pitirizanibe Kupemphererana

Mofanana ndi Paulo, tingapemphe ena kutipempherera. Pambali pa kupemphera nafe pamodzi, mabwenzi athu angatipempherere kwa Mlungu mwamseri, akumatitchula maina, kutchula vuto lathu, ndikupempha kuti atithandize. Ndipo thandizo lidzadza, popeza kuti ‘Yehova adziŵa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo.’​—2 Petro 2:9.

Mboni za Yehova zimene zimatitchula m’mapemphero awo zimakhalanso ndi ziyeso​—mwina zopsinja koposa zathu. Komabe, iwo amapereka nkhaŵa zathu pamaso pa Mfumu Yosatha, mwinamwake ngakhale kutigwetsera misozi. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 2:4; 2 Timoteo 1:3, 4.) Tiyenera kukhala oyamikira chotani nanga kaamba ka chimenechi! Chotero, kaamba ka chiyamikiro ndi zifukwa zina zimene tangokambitsiranazi, tiyeni tipemphererane.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena