Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Yohane Woyamba 4:18 amatiuza kuti: “Mulibe mantha m’chikondi; koma chikondi changwiro chitaya kunja mantha.” Koma Petro analemba kuti: “Kondani abale. Opani Mulungu.” (1 Petro 2:17) Kodi tingagwirizanitse motani mavesi aŵiriŵa?
Onse aŵiri Petro ndi Yohane anali atumwi amene anaphunzira mwachindunji kwa Yesu Kristu mwiniyo. Chotero tingakhale achidaliro kuti zimene analemba zimagwirizana. Ponena za mavesi ogwidwa mawu pamwambapa, mfungulo yake ndi yakuti atumwi aŵiriwo anali kulankhula mitundu iŵiri ya kuwopa.
Choyamba tiyeni tipende uphungu wa Petro. Monga momwe nkhani yake ikusonyezera, Petro anali kupereka kwa Akristu anzake chilangizo chouziridwa ponena za mmene iwo anayenera kuonera aja okhala ndi ulamuliro. M’mawu ena, iye anali kunena za lingaliro loyenera la kugonjera m’mbali zina. Chifukwa chake, iye analangiza Akristu kukhala ogonjera kwa amuna amene anali ndi malo aulamuliro m’maboma a anthu, monga mafumu kapena akazembe. (1 Petro 2:13, 14) Popitiriza, Petro analemba kuti: “Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, chitirani mfumu ulemu.”—1 Petro 2:17.
Malinga ndi nkhani yake, nkoonekeratu kuti pamene Petro ananena kuti Akristu ayenera ‘kuwopa Mulungu,’ anatanthauza kuti tiyenera kukhala ndi ulemu waukulu kwa Mulungu, mantha a kuwopa kuchimwira ulamuliro waukulu koposa.—Yerekezerani ndi Ahebri 11:7.
Bwanji ponena za mawu a mtumwi Yohane? Poyambirira mu 1 Yohane chaputala 4, NW, mtumwiyo anafotokoza kufunika kwake kwa kuyesa “mawu ouziridwa” onga ochokera kwa aneneri onyenga. Mawu amenewo ndithudi samachokera kwa Yehova Mulungu; amachokera ku dziko loipa kapena amasonyeza mzimu wake.
Mosiyana ndi zimenezo, Akristu odzozedwa ‘amachokera kwa Mulungu.’ (1 Yohane 4:1-6) Motero, Yohane analangiza kuti: “Okondedwa, tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu.” Mulungu ndiye anayamba kusonyeza chikondi—iye “anatuma Mwana wake akhale chiwombolo chifukwa cha machimo athu.” (1 Yohane 4:7-10) Kodi tiyenera kuchita motani?
Mwachionekere, tiyenera kukhala m’chigwirizano ndi Mulungu wathu wachikondi. Sitiyenera kuwopsezedwa naye kapena kuwopa kumfikira m’pemphero. Poyambirira Yohane anapereka uphungu wakuti: “Mtima wathu ukapanda kutitsutsa, tili nako kulimbika mtima mwa Mulungu; ndipo chimene chilichonse tipempha, tilandira kwa iye, chifukwa tisunga malamulo ake.” (1 Yohane 3:21, 22) Inde, chikumbumtima chabwino chimatipatsa kulimbika mtima pomfikira Mulungu popanda mantha a kumuwopa. Chifukwa cha chikondi, timakhala aufulu kulankhula, kapena kufikira Yehova m’pemphero. Mwa lingaliro limeneli, “mulibe mantha m’chikondi.”
Chotero tiyeni tigwirizanitse malingaliro aŵiriwo. Mkristu ayenera nthaŵi zonse kukhala ndi mantha aulemu kwa Yehova, chifukwa cha ulemu waukulu wa malo ake, mphamvu, ndi chilungamo. Koma timakondanso Mulungu monga Atate wathu ndipo timamva kukhala oyandikira kwa iye ndi aufulu kumfikira. M’malo mwa kukhala ndi mantha a kumuwopa, tiyenera kukhulupirira kuti tikhoza kumfikira, monga momwe mwana amakhalira womasuka kufikira kholo lake lachikondi.—Yakobo 4:8.