Mvetserani Bwinobwino
1 Pamafunika kudzilanga kuti timvetsere mwatcheru. Pamafunikanso kuti womvetsera akhale wofunitsitsa kuphunzira ndi kupindula ndi zimene akumvazo. N’chifukwa chake Yesu anagogomezera kufunika ‘koyang’anira mamvedwe anu.’—Luka 8:18.
2 Izi n’zofunika makamaka pamene tili pamisonkhano yampingo, yadera ndi yachigawo. Pamalo ameneŵa m’pomwe tiyenera kumvetsera mwatcheru. (Aheb. 2:1) Nazi mfundo zina zokuthandizani kumvetsera bwinobwino pamisonkhano yachikristu imeneyi.
◼ Dziŵani kufunika kwa misonkhano. Ili njira yaikulu imene ‘tikuphunzitsidwa ndi Yehova’ mwa “mdindo wokhulupirika.”—Yes. 54:13; Luka 12:42.
◼ Konzekerani pasadakhale. Pendani nkhani zimene zikakambidwa, ndipo tsimikizirani kuti mwatenga Baibulo lanu ndi buku limene mukaphunzire.
◼ Misonkhano ili m’kati, yesetsani kutchera khutu. Muyenera kupeŵa kulankhula anthu amene mwakhala nawo pafupi komanso kuyang’ana zimene ena akuchita. Musadzidodometse mwa kuganiza zimene mukachite mukatha msonkhano kapena kuganizira zinthu zina zaumwini.
◼ Lingalirani zimene zikukambidwazo. Dzifunseni kuti: ‘Kodi izi zikundikhudza motani? Kodi n’dzazigwiritsa ntchito liti?’
◼ Lembani mwachidule mfundo zazikulu ndi malemba. Izi zimakuthandizani kuika maganizo anu pazimene zikukambidwa ndipo zimathandiza kuti muzikumbukira mfundo zazikulu zimene mudzagwiritse ntchito nthaŵi ina.
3 Phunzitsani Ana Anu Kumvetsera: Ana amafunika malangizo auzimu. (Deut. 31:12) Kale pagulu la anthu a Mulungu “yense wakumva ndi kuzindikira” anayenera kutchera khutu poŵerengedwa Chilamulo. (Neh. 8:1-3) Ngati makolo amatengeka mtima ndi misonkhano komanso amamvetsera mwatcheru, mosapeneka ana awo adzachita zomwezo. Si bwino kutenga zidole kapena mabuku ojambulamo zithunzi zoti ana azikaseŵeretsa. Kupitapitanso kuchimbudzi kumadodometsa kumvetsera kwawo. Popeza “utsiru umangidwa mumtima mwa mwana,” makolo ayenera kuyesetsa kwambiri kuti ana awo akhazikika malo amodzi ndipo akumvetsera misonkhano.—Miy. 22:15.
4 Mwa kumvetsera bwinobwino, timasonyeza kuti ndifedi anzeru ndipo tikufuna ‘kuwonjezera kuphunzira.’—Miy. 1:5.