NYIMBO 42
Pemphero la Mtumiki wa Mulungu
Losindikizidwa
1. M’lungu Atate Wamphamvuyonse,
Dzina lanu liziyeretsedwadi.
Mumachita zomwe mwafuna.
Tikupempha Ufumu ubwere.
Pa nthawi yanu M’lungu
Mudzatidalitsatu.
2. Mumatipatsa zinthu zabwino,
Mphatso zoti sitikanazipeza.
Mumatipatsatu kuwala
Ndipo mumatipatsanso nzeru.
Tikukuthokozani
Ndinudi wachikondi.
3. Mavuto ndi ambiri m’dzikoli.
Tikupempha muzititonthozabe.
Tikuuzeni nkhawa zathu,
Muzitithandiza kupirira
Komanso kukwanitsa
Zomwe tinalonjeza.
(Onaninso Sal. 36:9; 50:14; Yoh. 16:33; Yak. 1:5.)