NYIMBO 46
Tikukuthokozani Yehova
Losindikizidwa
1. Tikukuthokozanitu Yehova.
Mumatipatsa kuwala kwanu.
Tikuthokoza mwayi wa pemphero
Kuti tinene mavuto athu.
2. Tikuthokoza potumiza Yesu
Amene anagonjetsa dziko.
Tikuthokozanso potithandiza
Kukwanitsa malonjezo athu.
3. Tikuthokoza chifukwa cha mwayi
Wolalikira za dzina lanu.
Tikuthokoza kuti posachedwa
Mavuto onsewa adzathadi.
(Onaninso Sal. 50:14; 95:2; 147:7; Akol. 3:15.)