NYIMBO 43
Pemphero Lothokoza
Losindikizidwa
1. Yehova tikufuna kuthokoza
Kudzera mupemphero lathuli.
Tizitumikira mofunitsitsa,
Timadziwa mumatithandiza.
Ndife anthu obadwa ndi uchimo
Chonde muzitikhululukira.
Tikuthokoza munatiwombola
Ndi dipo la mwana wanu Yesu.
2. Zikomo chifukwa munatikonda,
Munatikokeranso kwa inu.
Tiphunzitseni za inu Mulungu
Kuti nafe tizikukondani.
Zikomo chifukwa cha mzimu wanu,
Timalankhula molimba mtima.
Tizitumikira modzichepetsa.
Tikukuthokozani Yehova.
(Onaninso Sal. 65:2, 4, 11; Afil. 4:6.)