2 Mbiri
1 Solomo mwana wa Davide anapitiriza kukhala wamphamvu mu ufumu wake.+ Yehova Mulungu wake anali naye,+ ndipo anapitiriza kumukulitsa kuposa wina aliyense.+
2 Tsopano Solomo anaitanitsa Aisiraeli onse, atsogoleri a magulu a anthu 1,000,+ atsogoleri a magulu a anthu 100,+ oweruza,+ ndi akuluakulu onse a Isiraeli+ yense, amene anali atsogoleri a nyumba za makolo awo.+ 3 Kenako Solomo ndi mpingo wonsewo anapitira limodzi kumalo okwezeka a ku Gibeoni.+ Anapita kumeneko chifukwa ndi kumene kunali chihema chokumanako+ cha Mulungu woona, chimene Mose mtumiki+ wa Yehova anapanga m’chipululu. 4 Koma Davide anali atachotsa likasa+ la Mulungu woona ku Kiriyati-yearimu+ n’kukaliika kumalo amene iye anakonza,+ pakuti anali atamanga hema wa likasalo ku Yerusalemu.+ 5 Ndipo guwa lansembe lamkuwa+ limene Bezaleli+ mwana wa Uri mwana wa Hura+ anapanga, anali ataliika patsogolo pa chihema chopatulika cha Yehova. Choncho Solomo ndi mpingowo anafunsira paguwalo monga mwa nthawi zonse. 6 Ndiyeno kumeneko Solomo anapereka nsembe pamaso pa Yehova paguwa lansembe lamkuwalo limene linali kuchihema chokumanako. Iye anapereka nsembe zopsereza 1,000 paguwalo.+
7 Usiku wa tsiku limenelo, Mulungu anaonekera kwa Solomo ndi kumuuza kuti: “Tandiuza, ukufuna ndikupatse chiyani?”+ 8 Solomo atamva zimenezi anauza Mulungu kuti: “Inu ndinu amene mwasonyeza kukoma mtima kosatha kwa Davide bambo anga,+ ndipo mwandiika kukhala mfumu m’malo mwake.+ 9 Tsopano inu Yehova Mulungu, kwaniritsani+ lonjezo limene munapereka kwa Davide bambo anga. Pakuti ndinu amene mwandiika kukhala mfumu+ ya anthuwa amene ndi ochuluka kwambiri ngati fumbi lapadziko lapansi.+ 10 Mundipatse nzeru ndi luntha lodziwa zinthu+ kuti ndizitha kutsogolera+ anthuwa, pakuti ndani angaweruze anthu anu ochulukawa?”+
11 Pamenepo Mulungu anauza Solomo kuti: “Chifukwa chakuti zimenezi ndi zimene zili mumtima mwako+ ndipo sunapemphe katundu, chuma ndi ulemu kapenanso moyo wa anthu amene amadana nawe, sunapemphenso kuti ukhale ndi moyo masiku ambiri,+ koma wapempha kuti ukhale ndi nzeru ndi luntha lodziwa zinthu kuti uweruze anthu anga amene ndakupatsa kuti ukhale mfumu yawo,+ 12 upatsidwa nzeru ndi luntha lodziwa zinthu.+ Ndikupatsanso katundu, chuma, ndi ulemu zochuluka kwambiri kuposa zimene anali nazo mafumu amene anakhalako iwe usanakhale,+ ndiponso zoposa zimene aliyense wobwera pambuyo pako adzakhale nazo.”+
13 Zitatero, Solomo anabwerera ku Yerusalemu kuchokera kumalo okwezeka a ku Gibeoni,+ kuchihema chokumanako,+ ndipo anapitiriza kulamulira Isiraeli.+ 14 Ndiyeno Solomo anali kusonkhanitsa magaleta* ndi mahatchi* ankhondo, moti anakhala ndi magaleta 1,400 ndi mahatchi ankhondo 12,000.+ Zimenezi anali kuzisunga m’mizinda yosungiramo magaleta+ ndiponso pafupi ndi mfumuyo ku Yerusalemu. 15 Mfumuyo inachititsa kuti ku Yerusalemu siliva ndi golide akhale wochuluka kwambiri ngati miyala,+ ndiponso kuti matabwa a mkungudza akhale ochuluka kwambiri ngati mitengo yamkuyu+ ya ku Sefela.+ 16 Panalinso mahatchi amene Solomo anali kugula kuchokera ku Iguputo,+ ndipo gulu la amalonda a mfumu ndilo linali kugula mahatchiwo m’magulumagulu.+ 17 Nthawi ndi nthawi anali kugula galeta lochokera ku Iguputo pamtengo wa ndalama zasiliva 600. Hatchi anali kuigula pamtengo wa ndalama zasiliva 150. Umu ndi mmene mafumu onse a Ahiti ndi mafumu a ku Siriya+ anali kuchitira. Mafumuwa anali kugwiritsa ntchito amalondawo pogula zinthuzo.