Levitiko
1 Tsopano kuchokera m’chihema chokumanako,+ Yehova anaitana Mose ndi kulankhula naye kuti: 2 “Uza ana a Isiraeli+ kuti, ‘Munthu aliyense akafuna kupereka chiweto kwa Yehova kuti ikhale nsembe, azipereka ng’ombe, nkhosa kapena mbuzi.
3 “‘Ngati akupereka ng’ombe kuti ikhale nsembe yake yopsereza,+ azipereka yamphongo, yopanda chilema.+ Aziipereka kwa Yehova mwa kufuna kwake,+ pakhomo la chihema chokumanako. 4 Iye aziika dzanja lake pamutu pa nsembe yopserezayo ndipo idzalandiridwa+ kuti iphimbe machimo ake.+
5 “‘Kenako azipha ng’ombe yaing’onoyo pamaso pa Yehova. Ndiyeno ana a Aroni, ansembe,+ azibweretsa magazi ake ndi kuwawaza mozungulira paguwa lansembe,+ limene lili pakhomo la chihema chokumanako. 6 Nyama ya nsembe yopserezayo aziisenda chikopa ndi kuidula ziwaloziwalo.+ 7 Pamenepo ana a Aroni, ansembe, aziika moto paguwa lansembelo+ ndi kuyalapo nkhuni.+ 8 Ndipo ana a Aroni, ansembe, aziyala ziwalozo+ pankhuni zimene zili pamoto wa paguwa lansembepo. Aziyala ziwalozo pamodzi ndi mutu ndiponso mafuta. 9 Matumbo+ ake ndi ziboda zake azizitsuka ndi madzi. Akatero ansembe azitentha* nyama yonse paguwa lansembe kuti ikhale nsembe yopsereza. Imeneyi ndi nsembe yotentha ndi moto, yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+
10 “‘Ngati akupereka nkhosa+ kapena mbuzi kuti ikhale nsembe yake yopsereza, azipereka+ mwana wamphongo wopanda chilema.+ 11 Ndipo aziipha pamaso pa Yehova kumbali yakumpoto ya guwa lansembe. Akatero ana a Aroni, ansembe, aziwaza magazi ake mozungulira paguwa lansembe.+ 12 Kenako azidula nyamayo ziwaloziwalo. Azichotsa mafuta ake ndi mutu wake ndipo wansembe aziyala ziwalo zonsezo pankhuni zimene zili pamoto wa paguwa lansembepo.+ 13 Ndiyeno azitsuka matumbo+ ndi ziboda+ ndi madzi. Kenako wansembe azitenga nyama yonseyo ndi kuitentha+ paguwa lansembe. Imeneyi ndi nsembe yopsereza, nsembe yotentha ndi moto, yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+
14 “‘Koma ngati akupereka mbalame kuti ikhale nsembe yake yopsereza kwa Yehova, azipereka njiwa+ kapena ana a nkhunda.+ 15 Wansembe azibweretsa mbalameyo paguwa lansembe ndi kudula*+ mutu wake. Akatero aziitentha paguwa lansembe, koma magazi ake aziwakhetsera pansi pambali pa guwa lansembelo. 16 Azichotsa chitsokomero ndi nthenga zake ndi kuziponya potayira phulusa losakanizika ndi mafuta,+ chakum’mawa, pafupi ndi guwa lansembe. 17 Ndiyeno aziing’amba pakati cham’mapiko mwake, koma osailekanitsa.+ Kenako wansembe aziitentha paguwa lansembe pamwamba pa nkhuni zimene zili pamoto. Imeneyi ndi nsembe yopsereza,+ nsembe yotentha ndi moto, yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+