NKHANI YOPHUNZIRA 21
NYIMBO NA. 21 Muziika Ufumu Pamalo Oyamba
Tiziyembekezera Mzinda Umene Sudzawonongeka
“Tikufunitsitsa mzinda umene ukubwerawo.”—AHEB. 13:14.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi tiona mmene chaputala 13 cha buku la Aheberi chingatithandizire panopa komanso m’tsogolo.
1. Kodi Yesu ananena kuti n’chiyani chidzachitikire mzinda wa Yerusalemu?
KUTATSALA masiku ochepa kuti aphedwe, Yesu Khristu anafotokoza mwatsatanetsatane ulosi wina. Ulosiwu unakwaniritsidwa koyamba pamene Yerusalemu ndi kachisi zinawonongedwa. Iye anachenjeza kuti tsiku lina ‘magulu a nkhondo adzazungulira mzinda wa Yerusalemu.’ (Luka 21:20) Yesu anauza ophunzira ake kuti akadzaona magulu a nkhondowo adzathawe nthawi yomweyo. Magulu a nkhondo a Aroma ndi amene anakwaniritsa ulosiwu.—Luka 21:21, 22.
2. Kodi mtumwi Paulo anauza chiyani Akhristu a Chiheberi okhala ku Yudeya ndi Yerusalemu?
2 Kutangotsala zaka zochepa kuti asilikali a Aroma azungulire mzinda wa Yerusalemu, mtumwi Paulo analemba kalata yamphamvu yomwe panopa imadziwika kuti buku la Aheberi. Paulo anapereka kwa Akhristu a ku Yudeya ndi ku Yerusalemu malangizo omwe akanawathandiza kukonzekera zimene ankayembekezera. Iwo ankayembekezera kuti Yerusalemu adzawonongedwa. Akhristuwo ankafunika kukhala okonzeka kusiya nyumba komanso mabizinesi awo. Choncho ponena za mzinda wa Yerusalemu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Panopa tilibe mzinda wokhazikika, koma tikufunitsitsa mzinda umene ukubwerawo.”—Aheb. 13:14.
3. Kodi “mzinda wokhala ndi maziko enieni” n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani timauyembekezera?
3 Akhristu amene anachoka ku Yerusalemu ndi ku Yudeya ayenera kuti ankanyozedwa koma zimene anasankhazi zinathandiza kuti apulumuke. Masiku ano ifenso timanyozedwa chifukwa chakuti sitimadalira ndalama kapena kuyembekezera kuti anthu angathetse mavuto. N’chifukwa chiyani? Timadziwa kuti dzikoli likupita. Timafunitsitsa “mzinda wokhala ndi maziko enieni,” womwe ndi Ufumu wa Mulungu “umene ukubwerawo.”a (Aheb. 11:10; Mat. 6:33) Munkhaniyi tikambirana: (1) mmene malangizo a Paulo anathandizira Akhristu a m’nthawi yake kupitiriza kuyembekezera mzinda “umene ukubwerawo,” (2) mmene Paulo anawathandizira kukonzekera zinthu zimene ankayembekezera, komanso (3) mmene malangizo ake angatithandizire masiku ano.
TIZIKHULUPIRIRA MULUNGU CHIFUKWA SANGATISIYE
4. Kodi mzinda wa Yerusalemu unali wofunika bwanji kwa Akhristu?
4 Mzinda wa Yerusalemu unali wofunika kwambiri kwa Akhristu. Mpingo woyamba unakhazikitsidwa kumeneko mu 33 C.E., ndipo bungwe lolamulira linali komweko. Akhristu ambiri anali ndi nyumba komanso chuma mumzindawu. Koma Yesu anauza otsatira ake kuti adzayenera kuchoka mumzindawu ngakhalenso ku Yudeya.—Mat. 24:16.
5. Kodi Paulo anathandiza bwanji Akhristu kukonzekera zimene zinali m’tsogolo?
5 Pofuna kuthandiza Akhristu kukonzekera zimene zinkabwera, Paulo anawalimbikitsa kuti aziona mzinda wa Yerusalemu mmene Yehova ankauonera. Paulo anakumbutsa Akhristuwo kuti Yehova sankaonanso kachisi, ansembe komanso nsembe zimene zinkaperekedwa ku Yerusalemu ngati zopatulika. (Aheb. 8:13) Anthu ambiri mumzindawo anakana Mesiya. Kachisi wa ku Yerusalemu sanalinso likulu la kulambira koyera ndipo ankayembekezera kuwonongedwa.—Luka 13:34, 35.
6. N’chifukwa chiyani tinganene kuti malangizo a Paulo a pa Aheberi 13:5, 6 anali a pa nthawi yake?
6 Pa nthawi imene Paulo ankalembera kalata Aheberi, zinthu zinkayenda bwino mu Yerusalemu. Wolemba mbiri wina wa Chiroma ananena kuti pa nthawiyo, Yerusalemu unali “mzinda wotchuka kwambiri kum’mawa konse.” Ayuda ochokera m’madera osiyanasiyana ankapita mumzindawu chaka ndi chaka kukachita zikondwerero zosiyanasiyana. Izi zinachititsa kuti ku Yerusalemu kukhale chuma chambiri. Chifukwa cha zimenezi, n’zoonekeratu kuti Akhristu ena anali ndi chuma chambiri. Mwina n’chifukwa chake Paulo anawauza kuti: “Musamakonde ndalama koma muzikhutira ndi zomwe muli nazo pa nthawiyo.” Kenako ananena mawu a m’Malemba otsimikizira kuti Yehova sadzawasiya, akuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Werengani Aheberi 13:5, 6; Deut. 31:6; Sal. 118:6) N’chifukwa chiyani Akhristu a ku Yudeya ndi ku Yerusalemu anafunika kuwatsimikizira zimenezi? Chifukwa pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene analandira kalatayi, iwo ankafunika kusiya nyumba zawo, mabizinesi awo komanso zinthu zina. Ankafunika kupita kumadera ena n’kukayamba moyo watsopano.
7. N’chifukwa chiyani tiyenera kudalira kwambiri Yehova panopa?
7 Zimene tikuphunzirapo: Posachedwapa tikuyembekezera mapeto a dzikoli pa “chisautso chachikulu.” (Mat. 24:21) Mofanana ndi Akhristu a m’nthawi ya atumwi tiyenera kukhala maso komanso okonzeka. (Luka 21:34-36) Pachisautso chachikulu, mwina tidzafunika kusiya zinthu zathu zonse n’kumakhulupirira kuti Yehova sadzatisiya. Ngakhale panopa, chisautso chachikulu chisanayambe tikhoza kusonyeza ngati timadalira Yehova. Dzifunseni kuti, ‘Kodi zochita komanso zolinga zanga zimasonyeza kuti sindidalira chuma koma Mulungu yemwe analonjeza kuti adzatisamalira?’ (1 Tim. 6:17) Chitsanzo cha Akhristu a m’nthawi ya atumwi chingatithandize kukonzekera chisautso chachikulu. Koma pa “chisautso chachikulu” zinthu zidzakhala zovuta kwambiri kuposa kale lonse. Ndiye kodi tidzadziwa bwanji zoyenera kuchita chisautsochi chikadzayamba?
MUZIMVERA AMENE AKUTSOGOLERA
8. Kodi Yesu anapereka malangizo otani kwa ophunzira ake?
8 Patangopita zaka zochepa kuchokera pamene Paulo analembera Aheberi kalata, Akhristu anaona asilikali a Chiroma akuzungulira Yerusalemu. Izi zinasonyeza kuti mzinda wa Yerusalemu watsala pang’ono kuwonongedwa ndipo anafunika kuthawa. (Mat. 24:3; Luka 21:20, 24) Koma kodi akanathawira kuti? Yesu anangonena kuti: “Amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri.” (Luka 21:21) Popeza kuti kuderalo kunali mapiri ambiri, kodi iwo akanathawira mapiri ake ati?
9. N’chifukwa chiyani zinali zovuta kuti Akhristu adziwe mapiri oyenera kuthawirako? (Onaninso mapu.)
9 Ena mwa mapiri amene Akhristu akanathawirako anali awa: mapiri a ku Samariya, ku Galileya, ku Lebanoni, Phiri la Herimoni komanso mapiri a kutsidya lina la Yorodano. (Onani mapu.) Ena mwa mapiriwa ankaoneka ngati otetezeka. Mwachitsanzo, mzinda wa Gamla unali paphiri ndipo anali malo ovuta kufikako. Ayuda ena ankaganiza kuti mzinda umenewu unali malo abwino kuthawirako. Koma mumzindawu ndi mmene Ayuda ndi Aroma anadzamenyana koopsa ndipo anthu ambiri anaphedwa.b
Kunali mapiri ambiri omwe Akhristu akanathawirako. Koma si onse amene anali otetezeka (Onani ndime 9)
10-11. (a) Kodi Yehova ayenera kuti anapereka bwanji malangizo? (Aheberi 13:7, 17) (b) Kodi kutsatira malangizo a amene ankatsogolera kunathandiza bwanji Akhristu? (Onaninso chithunzi.)
10 Zikuoneka kuti Yehova anagwiritsa ntchito akulu mumpingo potsogolera Akhristu kuti adziwe koyenera kuthawira. Wolemba mbiri wina ananena kuti: “Anthu a mumpingo wa ku Yerusalemu analandira malangizo ochokera kwa Mulungu kudzera mwa akulu, owalamula kuti . . . achoke mumzindawo nkhondo isanayambe n’kuthawira kumzinda wa ku Pereya wotchedwa Pela.” Mzinda wa Pela unali wabwino kuti Akhristu athawireko. Mzindawu sunali kutali ndi Yerusalemu ndipo zinali zosavuta kufikako. Mumzindawu munkakhala anthu a mitundu ina choncho sunakhudzidwe pamene Ayuda ankamenyana ndi Aroma.—Onani mapu.
11 Akhristu amene anathawira kumapiri anatsatira malangizo Paulo akuti ‘tizimvera amene akutsogolera’ mumpingo. (Werengani Aheberi 13:7, 17.) Izi zinathandiza kuti apulumuke. Zimene zinachitika zinatsimikizira kuti Mulungu sanasiye anthu amene “ankayembekezera mzinda wokhala ndi maziko enieni,” womwe ndi Ufumu wa Mulungu.—Aheb. 11:10.
Ku Pela ndi kumene kunali kotetezeka (Onani ndime 10-11)
12-13. Kodi Yehova wakhala akutsogolera bwanji anthu ake pa nthawi yovuta?
12 Zimene tikuphunzirapo: Yehova amagwiritsa ntchito anthu amene akutsogolera kuti apereke malangizo kwa anthu ake. M’Baibulo muli zitsanzo za abusa angapo amene Yehova anawagwiritsa ntchito potsogolera anthu ake pa nthawi yovuta. (Deut. 31:23; Sal. 77:20) Masiku ano timaona umboni wakuti Yehova akupitirizabe kugwiritsa ntchito abusa amenewa.
13 Mwachitsanzo, mliri wa COVID-19 utayamba, abale ‘otsogolera’ anatipatsa malangizo oyenerera. Akulu analandira malangizo omwe anathandiza abale ndi alongo kuti apitirize kulambira Yehova. Pasanapite nthawi yaitali mliriwu utayamba, tinachita msonkhano wachigawo m’zilankhulo zoposa 500 kudzera pa intaneti, TV ndiponso wailesi. Anthu anapitirizabe kulandira chakudya chauzimu ndipo izi zinathandiza kuti tipitirizebe kukhala ogwirizana. Choncho kaya tikumana ndi mavuto otani m’tsogolomu, Yehova adzapitiriza kuthandiza abale otsogolera kuti adziwe zoyenera kuchita. Kuwonjezera kukhulupirira Yehova ndi kumvera ndi malamulo ake, kodi ndi makhalidwe enanso ati amene angatithandize kukonzekera chisautso chachikulu komanso kuti tidzachite zinthu mwanzeru pa nthawi yovutayi?
MUZIKONDA ABALE NDI ALONGO ANU KOMANSO KUWACHEREZA
14. Mogwirizana ndi Aheberi 13:1-3, kodi ndi makhalidwe ati amene Akhristu ankafunika kusonyeza, pamene Yerusalemu ndi kachisi zinatsala pang’ono kuwonongedwa?
14 Chisautso chachikulu chikadzayamba tidzafunika kusonyezana chikondi kuposa kale. Tidzafunika kutsanzira Akhristu omwe ankakhala ku Yerusalemu ndi ku Yudeya. Iwo nthawi zonse ankasonyezana chikondi. (Aheb. 10:32-34) Koma kutatsala zaka zochepa kuti Yerusalemu awonongedwe, Akhristuwo ankafunika kusonyezana chikondi kwambiri komanso kucherezana.c (Werengani Aheberi 13:1-3.) Ifenso tidzafunika kuchita zimenezi pa nthawi ya chisautso chachikulu.
15. N’chifukwa chiyani Akhristu a Chiheberi ankafunika kokonda anzawo komanso kuwalandira bwino pamene anathawa?
15 Asilikali a Chiroma anabwera kudzazungulira mzinda wa Yerusalemu ndipo mwadzidzidzi anabwerera. Pa nthawiyi Akhristu anathawa ndipo anali ndi zinthu zochepa. (Mat. 24:17, 18) Iwo ankafunika kudalirana kwambiri pamene ankathawira kumapiri komanso pamene ankayamba moyo watsopano. N’zosachita kufunsa kuti ambiri ankavutika ndipo ankafunika kuthandizidwa. Zimenezi zinapereka mwayi kwa Akhristu wosonyeza kuti amakondana kwambiri pothandizana komanso kugawana zimene ali nazo.—Tito 3:14.
16. Kodi tingasonyeze bwanji chikondi kwa Akhristu anzathu amene akuvutika? (Onaninso chithunzi.)
16 Zimene tikuphunzirapo: Chikondi chimatilimbikitsa kuti tizithandiza Akhristu anzathu omwe akuvutika. Anthu ambiri a Mulungu akhala akuthandiza abale ndi alongo awo omwe anathawa kwawo chifukwa cha nkhondo kapena ngozi zam’chilengedwe kuti azikhala ndi zinthu zofunika komanso azilambira Yehova. Mlongo wina wa ku Ukraine yemwe anathawa kwawo chifukwa cha nkhondo ananena kuti: “Yehova wakhala akugwiritsa ntchito abale potithandiza komanso kutitsogolera. Iwo anatilandira bwino komanso kutithandiza ku Ukraine, ku Hungary komanso kuno ku Germany.” Yehova amagwiritsa ntchito abale ndi alongo kuti alandire komanso kusamalira bwino anthu amene akumana ndi mavuto.—Miy. 19:17; 2 Akor. 1:3, 4.
Timafunika kuthandiza Akhristu amene athawa kwawo masiku ano (Onani ndime 16)
17. N’chifukwa chiyani panopa tiyenera kukonda Akhristu anzathu komanso kuwachereza?
17 Kutsogoloku tidzafunika kuthandizana kwambiri kuposa kale. (Hab. 3:16-18) Tingati Yehova akutiphunzitsa panopa kukhala achikondi komanso olandira bwino alendo. Makhalidwe amenewa adzafunika kwambiri pachisautso chachikulu.
ZIMENE ZICHITIKE M’TSOGOLO
18. Kodi tingatsanzire bwanji Akhristu a Chiheberi?
18 Akhristu omwe anathawira kumapiri anapulumuka pamene Yerusalemu ankawonongedwa. Iwo atathawa mumzindawu, Yehova sanawasiye. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Sitingadziwiretu zonse zimene zidzachitike m’tsogolomu. Koma Yesu anatiuza kuti tiyenera kukhala okonzeka kumvera. (Luka 12:40) Tilinso ndi malangizo omwe Paulo anapereka kwa Akhristu a Chiheberi. Malangizowa ndi othandiza panopa ngatinso mmene zinalili pa nthawiyo. Yehova watitsimikiziranso kuti sangatisiye kapena kutitaya ngakhale pang’ono. (Aheb. 13:5, 6) Tiyeni tipitirize kuyembekezera Ufumu wa Mulungu, umene ndi mzinda womwe udzakhalapo mpaka kalekale. Tikatero tidzasangalala ndi madalitso amene Ufumuwo udzabweretse.—Mat. 25:34.
NYIMBO NA. 157 Kudzakhala Mtendere
a Kale, mizinda yambiri inkalamuliridwa ndi mafumu. Mizinda yotereyi inkatchedwa kuti ufumu.—Gen. 14:2.
b Izi zinachitika mu 67 C.E., pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Akhristu anathawa ku Yerusalemu ndi ku Yudeya.
c Mawu amene anawamasulira kuti “kukonda abale” amanena za chikondi cha pakati pa anthu apachibale. Koma Paulo anawagwiritsa ntchito ponena za kugwirizana komwe kumakhalapo pakati pa Akhristu mumpingo.