Maulaliki Acitsanzo
Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo pa Ciŵelu Coyamba mu September
“Muli bwanji? Tikucezela anthu mwacidule kuti tiwaonetse cimene cingathandize mabanja kukhala acimwemwe. Malinga ndi kuona kwanu, kodi n’ciani cimacititsa kuti mabanja asakhale acimwemwe?” [Yembekezani yankho.] Muonetseni nkhani ili pacikuto cothela ca Nsanja ya Mlonda ya September 1. Ndiyeno kambilanani naye nkhani ili pansi pa funso loyamba ndi kuŵelenga lemba limodzi. Kenako, m’gaŵileni magazini ndi kupangana naye kuti mukabwelenso kudzakambilana funso lotsatila.
Nsanja ya Olonda September 1
“Tikucezela anthu kaamba kakuti anthu ambili m’dela lathu amadzifunsa cifukwa cake Mulungu walolela mavuto ambili conco. Kodi inunso munayamba mwadzifunsapo pankhani imeneyi? [Yembekezani yankho.] N’zokondweletsa kudziŵa kuti Baibo inatilonjeza kuti idzafika nthawi imene kulila komanso kumva zoŵaŵa kudzatha. [Ŵelengani Chivumbulutso 21:4.] Magazini iyi ifotokoza zifukwa zisanu zoonetsa cifukwa cake mavuto aculuka conco. Ifotokozanso zimene Baibo imakamba za mmene Mulungu adzathetsela mavuto.”
Galamukani! September
“Kodi muganiza kuti ngati amuna ndi akazi amene ali pabanja atsatila malangizo a m’Baibo awa, mabanja ao angakhale olimba? [Welengani Akolose 3:13. Yembekezani ayankhe.] Nkhani iyi ifotokoza mfundo za m’Baibo zimene zingathandize anthu amene ali pabanja kuti azikhululukilana.” Gwilitsilani nchito nkhani imene ili patsamba 6.