Maulaliki Acitsanzo
Kuyambitsa Maphunzilo a Baibulo pa Ciŵelu Coyamba mu May
“Tikukambilana ndi anthu mwacidule funso locititsa cidwi ili. [Muonetseni funso loyamba limene lili kucikuto cothela ca Nsanja ya Mlonda ya May 1.] Mugayankhe bwanji?” Yembekezelani ayankhe. Ndiyeno kambilanani naye mfundo zimene zili pansi pa funso, muŵelengenso lemba limodzi. Mugaŵileni magazini, ndi kupangana naye kuti mudzabwelanso kudzakambilana funso lotsatila.
Nsanja ya Mlonda May 1
“Tikuceza ndi anthu mwacidule cifukwa ambili amasangalala kudziŵa zimene zidzacitika mtsogolo. Mukaganizila za mtsogolo, kodi inu mumamva bwanji? Zimakupatsani cidalilo kapena zimakudetsani nkhawa? [Yembekezelani ayankhe. Ndiyeno ŵelengani malemba amene ali pamutu wakuti “Zimene Mulungu waulula ponena za mtsogolo.”] Magazini iyi ifotokoza zinthu zina zimene Mulungu wanena kuti zidzacitika ndiponso cifukwa cake tiyenela kukhala otsimikizila kuti zidzacitikadi.”
Galamukani! May
“Tikuceza ndi anthu mwacidule kukambilana nao za mmene angathetsele vuto la kupanikizika. Kodi muona kuti masiku ano anthu ndi opanikizika kwambili kuposa kale? [Yembekezelani ayankhe.] Ambili apeza kuti malangizo a m’Baibulo amawathandiza kuthetsa vuto la kupanikizika. Onani citsanzo ici. [Ŵelengani Mateyu 6:34.] Magazini iyi ifotokoza mmene mfundo za m’Baibulo zingatithandizile kuthetsa zinthu zinai zofala zimene zimacititsa kuti tikhale opanikizika.”
Cidziŵitso: Magaziniyi ingadzutse cidwi capadela kwa anthu a malonda.