NKHANI YOPHUNZILA 12
NYIMBO 77 Kuwala m’Dziko la Mdima
Pewani Mdima— Khalanibe m’Kuwala
“Poyamba munali mdima, koma tsopano ndinu kuwala.”—AEF. 5:8.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Zomwe tingaphunzile ku mawu akuti “mdima,” komanso “kuwala” amene Paulo anaseŵenzetsa mu Aefeso caputa 5.
1-2. (a) Kodi mtumwi Paulo anali mu mkhalidwe wotani pamene anali kulembela kalata Aefeso? (b) Tikambilane mafunso ati m’nkhani ino?
PAMENE Paulo anali pa ukaidi wosacoka panyumba ku Roma, anafunitsitsa kulimbikitsa Akhristu anzake. Sakanatha kuwayendela kunyumba zawo. Conco anawalembela makalata. Imodzi mwa makalata amenewo analembela Aefeso ca m’ma 60 kapena 61 C.E.—Aef. 1:1; 4:1.
2 Pafupifupi zaka 10 m’mbuyomo, Paulo anakhalako ku Roma kwa kanthawi akulalikila uthenga wabwino. (Mac. 19:1, 8-10; 20:20, 21) Anali kuwakonda ngako abale na alongo ake, ndipo anafuna kuwathandiza kuti akhalebe okhulupilika kwa Yehova. Koma n’cifukwa ciyani analembela Akhristu odzozedwa nkhani ya mdima na kuwala? Nanga kodi Akhristu onse angaphunzile ciyani pa uphungu umenewu? Tiyeni tione mayankho a mafunso amenewa.
KUCOKA MU MDIMA KULOŴA M’KUWALA
3. Ni mawu ophiphilitsa ati amene Paulo anaseŵenzetsa m’kalata yake kwa Aefeso?
3 Paulo analembela Akhristu a ku Efeso kuti: “Poyamba munali mdima, koma tsopano ndinu kuwala.” (Aef. 5:8) Pa lembali, Paulo anagwilitsa nchito mawu akuti mdima na kuwala pofotokoza zinthu ziŵili zosiyana kwambili. Tiyeni tikambilane cifukwa cake Paulo analemba kuti Aefeso ‘poyamba anali mdima.’
4. Kodi Aefeso anali mumdima wa cipembedzo m’lingalilo lotani?
4 Mdima wa cipembedzo. Aefeso amene Paulo anawalembela kalatayi anali mu ukapolo ku ziphunzitso za cipembedzo conyenga asanaphunzile coonadi n’kukhala Akhristu. Ndipo anali kukhulupilila zamatsenga. Mumzinda wa Efeso ni mmene munali kacisi wochuka wa mulungu wabodza dzina lake Atemi. Anthu ambili pa nthawiyo anali kunena kuti kacisi ameneyu anali mmodzi mwa zinthu 7 zocititsa cidwi zimene anthu anapanga. Anthu ambili anali kupita kumeneko anali ozama m’kulambila mafano. A zamalonda anali kupanga zifanizilo za Atemi na kacisi wochuka uja, ndipo anali kupha nazo ndalama zambili. (Mac. 19:23-27) Kuwonjezela apo, anthu ambili mumzindawo anali ochuka na zamatsenga.—Mac. 19:19.
5. Kodi Aefeso anali mumdima wa makhalidwe m’lingalilo lotani?
5 Mdima wa makhalidwe. Mzinda wa Efeso unali wochuka cifukwa ca ciwelewele na makhalidwe ena onyansa. Anthu ambili anali kukonda kukamba nkhani zotukwana m’mabwalo a maseŵelo ngakhale pa zikondwelelo za cipembedzo. (Aef. 5:3) Iwo ‘sanali kuthanso kuzindikila makhalidwe abwino.’ Izi zingotiuza kuti iwo “sanali kudzimvela cisoni pa khalidwe lawo.” (Aef. 4:17-19) Ndipo asanaphunzile miyeso ya Yehova ya cabwino na coipa, cikumbumtima cawo sicinali kuwaimba mlandu pa makhalidwe awo oipa. Sanali kudelanso nkhawa mmene zocita zawo zinali kukhudzila Yehova. Ndiye cifukwa cake Paulo anawauza kuti “alinso mumdima wa maganizo otalikilana ndi moyo wa Mulungu.”
6. N’cifukwa ciyani mtumwi Paulo anauza Aefeso kuti “tsopano ndinu kuwala”?
6 Komabe ena mwa Aefeso sanakhalebe mumdima. Paulo anawalembela kuti “tsopano ndinu kuwala mogwilizana ndi Ambuye.” (Aef. 5:8) Iwo anali atalandila kuwala kwa coonadi ca m’Malemba. (Sal. 119:105) Anasiya miyambo ya cipembedzo conyenga, komanso makhalidwe oipa. Anayamba ‘kutsanzila Mulungu,’ ndipo anali kuyesetsa mmene angathele kulambila Yehova, komanso kum’kondweletsa.—Aef. 5:1.
7. Kodi tikufanana motani na Akhristu ambili a ku Efeso?
7 Mofananamo, tisanaphunzile coonadi tinali mu mdima wa cipembedzo komanso wa makhalidwe oipa. Ena a ife tinali kukondwelela maholide a zipembedzo zonyenga. Ndipo ena anali kukhala umoyo wa makhalidwe otayilila. Koma tinasintha titaphunzila miyeso ya Yehova ya cabwino na coipa. Tinayamba kukhala umoyo woyendela miyeso yake. Mwa ici, talandila madalitso oculuka. (Yes. 48:17) Komabe, si capafupi kukhalabe kunja kwa mdima umene tinasiya, na kupitiliza ‘kuyendabe ngati ana a kuwala.’ Conco, tingacite bwanji zimenezi?
Image digitally reproduced with the permission of the Papyrology Collection, Graduate Library, University of Michigan, P.Mich.inv. 6238. Licensed under CC by 3.0
Zimene Paulo analembela Aefeso ni ulangizi wacikondi umene tingaseŵenzetse masiku ano (Onani ndime 7)b
PEWANI MDIMA
8. Malinga na Aefeso 5:3-5, kodi Aefeso anafunika kupewa ciyani?
8 Ŵelengani Aefeso 5:3-5. Kuti Akhristu a ku Efeso apeweletu mdima wa makhalidwe oipa, anafunika kupitilizabe kukaniza makhalidwe amene Yehova amadana nawo. Izi zinaphatikizapo kupewa zaciwelewele komanso nkhani zotukwana. Paulo anakumbutsa Aefeso kuti ngati sangapewe zinthu zimenezi, “sadzaloŵa mu Ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu.”
9. N’cifukwa ciyani tiyenela kupewa ciliconse cimene cingatipangitse kucita ciwelewele?
9 Nafenso tiyenela kupewa kukodwa mu msampha wocita “nchito zosapindulitsa za mu mdima.” (Aef. 5:11) Zocitika zaonetsa kuti ngati munthu amaonelela zaciwelewele mobweleza-bweleza, amazimvetsela, kapena amakonda kukamba nkhani zimenezi, cimakhala capafupi kwa iye kugwela m’chimo. (Gen. 3:6; Yak. 1:14, 15) M’dziko lina, kagulu ka abale kanatsegula tsamba la mcezo n’kuyamba kulembelana mauthenga. Ambili a iwo anayamba mwa kukambilana zinthu zauzimu, koma m’kupita kwa nthawi anayamba kukambilana nkhani zosakondweletsa Yehova. Anayamba kukambilana nkhani za kugonana. Ambili mwa abale amenewa pambuyo pake anaulula kuti makambidwe odetsa a m’gululo ni amene anawatsogolela kucita ciwelewele.
10. Kodi Satana amayesa kutigwila m’maso motani? (Aefeso 5:6)
10 Dziko la Satanali limayesa kutigwila m’maso. Limafuna kutipangitsa kukhulupilila kuti zinthu zimene Yehova amanena kuti n’zoipa komanso zodetsa, si zoipa ngakhale pang’ono. (2 Pet. 2:19) Zimenezi si zodabwitsa. Amodzi mwa macenjela amene Mdyelekezi wagwilitsa nchito kwa nthawi yaitali ni kusokoneza anthu kuti asathe kuzindikila cimene zili cabwino na coipa. (Yes. 5:20; 2 Akor. 4:4) Ndiye cifukwa cake mafilimu ambili, mapulogilamu a pa TV, na mawebusaiti, amalimbikitsa maganizo osemphana na miyeso yolungama ya Yehova. Satana amafuna kutipangitsa kukhulupilila kuti makhalidwe odetsa ni abwino-bwino, osangalatsa komanso si ovulaza.—Ŵelengani Aefeso 5:6.
11. Kodi cocitika ca Angela citionetsa bwanji kufunika koseŵenzetsa uphungu wa pa Aefeso 5:7? (Onaninso cithunzi.)
11 Satana amafuna kuti tiziceza na anthu amene angatilepheletse kutsatila miyeso ya Yehova. Ndiye cifukwa cake ponena za anthu ocita zoipa pamaso pa Mulungu, Paulo analangiza Aefeso kuti “musamacite zimene iwo amacita.” (Aef. 5:7) Komabe tizisamala kwambili ngakhale kuposa Aefeso. Zili conco cifukwa mosiyana na mmene zinalili kwa Aefeso, anthu amene timaceza nawo si okhawo amene timaceza nawo pamaso-m’pamaso ayi. Amaphatikizapo ngakhale aja amene timaceza nawo pa masamba amcezo. Mlongo Angelaa wa ku Asia anazindikila kuopsa kwa masamba amcezo. Iye anati, “Angakhale msampha, ndipo angasinthiletu maganizo a munthu. N’nafika poona kuti zilibe vuto kukhala paubwenzi na anthu amene salemekeza mfundo za m’Baibo. Pothela pake, n’nayamba kuona kuti palibe vuto kukhala umoyo wosakondweletsa Yehova.” N’zoyamikilika kuti akulu acikondi anam’thandiza Angela kupanga masinthidwe ofunikila. Ndiyeno iye anati, “Tsopano nimadzaza maganizo anga na zinthu zauzimu osati zinthu za pa masamba amcezo.”
Kuti tipitilizebe kutsatila miyeso ya Yehova, zimadalila kwambili mabwenzi amene timasankha (Onani ndime 11)
12. N’ciyani cingatithandize kutsatilabe miyeso ya Yehova ya cabwino na coipa?
12 Tikanize maganizo a dziko akuti makhalidwe oipa ni ovomelezeka. Cifukwa ciyani? Tidziŵa kuti ni oipa. (Aef. 4:19, 20) Tingacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi nimayesetsa kupewa maceza osafunika na anthu a kunchito, m’kalasi, kapena anthu ena osalemekeza miyeso yolungama ya Yehova? Kodi nimatsatila miyeso ya Yehova molimba mtima ngakhale kuti ena anganene kuti sindine wololela nikacita zimenezi?’ Monga yaonetsela 2 Timoteyo 2:20-22, tiyenelanso kusamala ngako posankha mabwenzi a pamtima ngakhale mumpingo. Tizikumbukila kuti ena sangatithandize kukhalabe okhulupilika mu utumiki wathu kwa Yehova.
MUZIYENDA “NGATI ANA A KUWALA”
13. Kodi ‘kuyendabe ngati ana a kuwala’ kutanthauza ciyani? (Aefeso 5:7-9)
13 Paulo analimbikitsa Akhristu a ku Efeso kuti apitilize kukaniza mdima, komanso kuti ‘ayendebe ngati ana a kuwala.’ (Ŵelengani Aefeso 5:7-9.) Kodi izi zitanthauza ciyani? Mwacidule tinganene kuti zitanthauza kuti nthawi zonse tiyenela kucita zinthu monga Akhristu enieni. Njila imodzi yocitila zimenezi ni kuŵelenga na kuphunzila Baibo mwakhama pamodzi na zofalitsa zozikika m’Baibo. Cina, popeza kuti Yesu ndiye “kuwala kwa dziko,” m’pofunika kwambili kutsatila citsanzo cake, komanso zimene anaphunzitsa.—Yoh. 8:12; Miy. 6:23.
14. Kodi mzimu woyela ungatithandize motani?
14 Timafunikilanso thandizo la mzimu wa Mulungu kuti tipitilize kucita zinthu “ngati ana a kuwala.” Cifukwa ciyani? Cifukwa si copepuka kukhalabe woyela m’dziko lino lodzala na makhalidwe oipa. (1 Ates. 4:3-5, 7, 8) Mzimu woyela ungatithandize kugonjetsa maganizo a m’dzikoli amene amasemphana na kaganizidwe ka Mulungu. Mzimuwo ungatithandizenso kubala cipatso “ciliconse cabwino ndi ciliconse colungama.”—Aef. 5:9.
15. Ni njila ziti zimene tingalandilile mzimu woyela? (Aefeso 5:19, 20)
15 Njila imodzi imene tingalandile mzimu woyela ni kuupempha. Yesu ananena kuti Yehova “adzapeleka mowolowa manja mzimu woyela kwa amene akum’pempha.” (Luka 11:13) Timalandilanso mzimu woyela tikamatamanda Yehova capamodzi pa misonkhano yathu. (Ŵelengani Aefeso 5:19, 20.) Cisonkhezelo cabwino cimene mzimu woyela umakhala naco pa ife cimatithandiza kukhala na umoyo wokondweletsa Mulungu.
16. N’ciyani cingatithandize kupanga zisankho zanzelu (Aefeso 5:10, 17)
16 Tikafunika kupanga cisankho cofunika kwambili, tiyenela “kuzindikila cifunilo ca Yehova,” na kucita zinthu mogwilizana na cifuniloco. (Ŵelengani Aefeso 5:10, 17.) Tikamafufuza na kupeza mfundo za m’Baibo zothandiza pa cisankho cimene tifuna kupanga, kwenikweni timakhala tikufunafuna maganizo a Mulungu pa nkhaniyo. Ndipo tikagwilitsa nchito mfundo zake, timapanga zisankho zabwino.
17. Kodi tingatani kuti tidzigwilitsa nchito bwino nthawi yathu? (Aefeso 5:15, 16) (Onaninso cithunzi.)
17 Paulo analangizanso Akhristu a ku Efeso kuti aziseŵenzetsa nthawi yawo mwanzelu. (Ŵelengani Aefeso 5:15, 16.) Mdani wathu Satana, “Woipayo,” amafuna kuticenjeneka na kufuna-funa zinthu za m’dzikoli n’colinga cakuti tizisoŵelatu nthawi yotumikila Mulungu. (1 Yoh. 5:19). Cingakhale capafupi kwa Mkhristu kutsogoza zakuthupi, maphunzilo, kapena nchito m’malo moseŵenzetsa mipata imene ilipo yotumikila Yehova. Zotelezi zikacitika, zingaonetse kuti munthu wayamba kuyendela maganizo a m’dzikoli. N’zoona kuti zinthu zimenezi si zoipa kwenikweni. Koma si ndiye zomwe tiyenela kutsogoza pa umoyo wathu. Kuti tiyende “ngati ana a kuwala,” tiyenela ‘kugwilitsa nchito bwino nthawi yathu’ poika maganizo athu pa zinthu zofunika kwambili.
Akhristu a ku Efeso analimbikitsidwa kuseŵenzetsa nthawi yawo mwanzelu (Onani ndime 17)
18. Kodi m’bale Donald anatenga masitepe otani kuti aziseŵenzetsa bwino nthawi yake?
18 Khalani chelu kuti muzindikile mpata uliwonse wotumikila Yehova mokwanila. Izi n’zimene m’bale Donald wa ku South Africa anacita. Iye anati, “Ninaganizila za mmene zinthu zinalili pa umoyo wanga na kucondelela Yehova kuti anithandize kucita zambili mu utumiki wake. Ninam’pempha kuti nipeze nchito imene inganipatse mpata woculuka wolalikila. Na thandizo la Yehova, n’naipezadi nchitoyo. Kenako, ine na mkazi wanga tinayamba kutumikila Yehova mu utumiki wa nthawi zonse.”
19. Tingapitilize bwanji kuyenda “ngati ana a kuwala”?
19 Kalata ya Paulo kwa Aefeso inawathandiza kwambili paumoyo wawo wa Cikhristu. Ndipo upangili wouzilidwa umenewu nafenso ungatithandize. Monga taonela, ungatithandize kusankha zosangalatsa mwanzelu, komanso kusankha mabwenzi abwino. Ungatikolezelenso kuti tiziŵelenga Mawu a Mulungu nthawi zonse kuti kuwala kwa coonadi kupitilize kutitsogolela m’zocita zathu zonse. Ndipo upangiliwu wagogomezanso kufunika kwa mzimu woyela umene umatithandiza kukhala na makhalidwe abwino. Kugwilitsa nchito zimene Paulo analemba kudzatithandiza kupanga zisankho zanzelu, zimene n’zogwilizana na maganizo a Yehova. Popitiliza kucita zinthu zimenezi tidzatha kupewa mdima wa m’dzikoli, na kukhalabe mu kuwala!
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
Kodi “mdima” na “kuwala” kochulidwa pa Aefeso 5:8 kuimila ciyani?
Tingaupewe bwanji “mdima”?
Tingapitilize bwanji kuyenda “ngati ana a kuwala”?
NYIMBO 95 Kuwala Kuwonjezeleka
a Maina ena asinthidwa.
b MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Pacithunzi pakuonetsa kalata yamakedzana ya mtumwi Paulo kwa Aefeso.