LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 December masa. 14-19
  • Tengelani kudzicepetsa kwa Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tengelani kudzicepetsa kwa Yehova
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • YEHOVA NDI WOFIKILIKA
  • YEHOVA NDI WOLOLELA
  • YEHOVA NDI WOLEZA MTIMA
  • YEHOVA AMALEMEKEZA ANTHU ODZICEPETSA
  • Tengelani Kaganizidwe ka Yehova ndi Yesu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Pezani Cimwemwe Coculuka Cimene Cimabwela Cifukwa Copatsa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 December masa. 14-19

NKHANI YOPHUNZILA 50

NYIMBO 48 Kuyenda ndi Yehova Tsiku na Tsiku

Tengelani Kudzicepetsa kwa Yehova

“Muzitsanzila Mulungu, monga ana ake okondedwa.”​—AEF. 5:1.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Tione njila zinai zokhalila odzicepetsa potengela Yehova.

1. N’cifukwa ciani kudzicepetsa kwa Yehova n’kocititsa cidwi?

KODI mumaona khalidwe la kudzicepetsa pakati pa olamulila masiku ano? Mwacionekele, ai. Koma n’zocititsa cidwi kuti Yehova, yemwe ndi wamphamvuzonse, ndi wodzicepetsa. (Sal. 113:​5-8) Iye ndi wodzicepetsa kuposa munthu wina aliyense. Ndipo alibiletu khalidwe lodzikuza ngakhale pang’ono. M’nkhani ino, tione makhalidwe anai ocititsa cidwi a Yehova, ndipo tikambilana mmene khalidwe lililonse limaonetsela kuti ndi wodzicepetsa kwambili. Tionenso mmene Yesu anaonetsela kudzicepetsa potengela Atate wake. Kukambilana makhalidwe amenewa kutithandiza kumuyandikila kwambili Yehova. Kutithandizenso kukhala odzicepetsa kwambili potengela Yehova.

YEHOVA NDI WOFIKILIKA

2. Kodi lemba la Salimo 62:8 limatiuzanji za Yehova? (Onaninso cithunzi.)

2 Anthu onyada nthawi zambili sakhala ofikilika. Amacita zinthu m’njila imene imapangitsa kuti ena asamamasuke kuwafikila kapena kuti azingowapewelatu. Izi n’zosiyana kwambili ndi mmene Yehova alili! Cifukwa cakuti Atate wathu wakumwamba ndi wodzicepetsa, iye amatiuza kuti tizim’fikila n’kumuuza zinthu zimene zikutidetsa nkhawa. (Welengani Salimo 62:8.) Mofanana ndi tate wacikondi amene amakhala wokonzeka kumvetsela zimene zikudetsa nkhawa ana ake, Yehova amamvetsela mapemphelo a alambili ake. Iye anaonetsetsa kuti ena mwa mapemphelo amenewa alembedwa m’Baibo. Izi zionetsa kuti Yehova ndi wofikilika kwambili. (Yos. 10:​12-14; 1 Sam. 1:​10-18) Koma bwanji ngati nthawi zina timaopa kupemphela kwa Yehova cifukwa ca zolakwa zathu?

Tate akumvetsela mwachelu pamene mwana wake akum’fotokozela zimene zacitika kuti aphwanye ciwiya coikamo maluwa pamene anali kusewela ndi kandeke.

Potengela citsanzo ca Yehova ca kudzicepetsa, tate akumvetsela mwana wake amene waphwanya ciwiya coikamo maluwa pomwe anali kusewela (Onani ndime 2)


3. Tidziwa bwanji kuti Yehova amafuna kuti tizipemphela kwa iye kawili-kawili?

3 Tingapemphelebe kwa Yehova ngakhale pamene tikuona ngati ndife osayenela cikondi cake. N’cifukwa ciani tikutelo? M’fanizo la mwana wolowelela, Yesu anayelekezela Yehova ndi tate wacikondi amene mwana wake wolapa anadziona ngati wosayenela kulandilidwanso. Kodi tateyo anatani mwana wake atabwelela kunyumba? Yesu anati tateyo atangomuona mwanayo “anamuthamangila ndi kumukumbatila ndipo anamupsompsona mwacikondi.” (Luka 15:​17-20) Yehova ali ngati tateyo. Cifukwa cakuti ndi wodzicepetsa, akangomva mapemphelo a anthu amene akudziimba mlandu, kapena olemedwa ndi nkhawa, amamvetsela mosamala kwambili. (Maliro 3:​19, 20) Ndipo cifukwa cowamvela cifundo, Yehova amawathamangila, titelo kunena kwake, kuti akawatonthoze ndi kuwatsimikizila kuti amawakonda. (Yes. 57:15) Kodi amacita bwanji zimenezi? Nthawi zambili, amagwilitsa nchito anthu amene amam’konda monga akulu, acibale athu omwe ndi Mboni, komanso alambili anzathu. (Yak. 5:​14, 15) Yehova amatithandiza mwa njila imeneyi cifukwa amafuna kuti tizimasuka naye.

4. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anali wofikilika?

4 Kodi Yesu anatengela bwanji citsanzo ca Atate wake? Mofanana ndi Atate wake, nayenso Yesu ndi wodzicepetsa. N’cifukwa cake ali padziko lapansi, anthu anali kumasuka kum’fikila. Iwo sanali kuopa kum’funsa mafunso. (Maliko 4:​10, 11) Akawapempha kuti afotokoze maganizo ao pankhani inayake, anali kukambapo momasuka. (Mat. 16:​13-16) Ndipo akalakwitsa zinazake, sanali kucita mantha cifukwa anali kudziwa kuti Yesu ndi wokoma mtima, wacifundo, komanso woleza mtima. (Mat. 17:​24-27) Cifukwa cakuti anatengela ndendende citsanzo ca Atate wake, Yesu anathandiza ophunzila ake kum’dziwa bwino Yehova. (Yoh. 14:9) Poona citsanzo ca Yesu, iwo anazindikila kuti Yehova sanali ngati atsogoleli acipembedzo a pa nthawiyo omwe anali ankhanza, onyada, ndi odzitukumula. Koma anaona kuti Yehova ndi wodzicepetsa komanso wofikilika.

5. N’cifukwa ciani anthu sabvutika kutifikila tikakhala odzicepetsa?

5 Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yehova? Tikakulitsa khalidwe la kudzicepetsa, tidzakhala ofikilika kwambili. Kudzicepetsa kudzatithandiza kupewa makhalidwe monga kaduka, kunyada, ndi kusakhululuka. Makhalidwewa angapangitse anthu ena kulephela kutifikila. Koma kudzicepetsa kudzatithandiza kukhala okoma mtima, oleza mtima, komanso okhululuka. Makhalidwe amenewa adzapangitsa ena kukhala omasuka kutifikila. (Akol. 3:​12-14) Akulu maka-maka, ayenela kuyesetsa kukhala ofikilika. Koma kuti akhaledi ofikilika, ayenela kumaonekela kwa ofalitsa. Izi zitanthauza kuti ayenela kuyesetsa kumapezeka pa misonkhano yampingo ya pamaso-m’pamaso. Ayenela kukonda misonkhanoyi kuposa ya pa vidiyokomfalensi. Cinanso, iwo ayenela kumalalikila kunyumba ndi nyumba ndi abale ndi alongo mmene angathele. Ofalitsa akawadziwa bwino akulu, sadzamangika kuwafikila akafunikila thandizo.

YEHOVA NDI WOLOLELA

6-7. Fotokozani zitsanzo zoonetsa kuti Yehova anaonetsa kuti ndi wololela atumiki ake atam’pempha zinazake.

6 Anthu onyada ambili sakhala ololela pocita zinthu ndi anthu ena. Koma izi n’zosiyana kwambili ndi Yehova. Pokhala wodzicepetsa, iye ndi wololela ngakhale kuti amaposa aliyense pa ciliconse. Ganizilani mmene anacitila zinthu ndi Miriamu mlongo wake wa Mose. Iye pamodzi ndi Aroni anadandaula motsutsana ndi Mose, amene anali kuimilako Yehova. Mwa kucita zimenezi, Miriamu anaonetsa kusalemekeza Yehova. Conco, Yehova anam’kwiyila ndipo anam’kantha ndi khate. Kenako, Aroni anapempha Mose kuti amuthandize Miriamu . Ndipo Mose anacondelela Yehova kuti acilitse Miriamu. Kodi Yehova anatani? Mulungu sanangoima nga! nga! nga! pa cigamulo cake. Popeza kuti Yehova ndi wodzicepetsa, anaonetsa kulolela mwa kum’cilitsa Miriamu.​—Num. 12:​1-15.

7 Yehova anacitanso zinthu modzicepetsa ndi Mfumu Hezekiya. Kudzela mwa mneneli Yesaya, Yehova anauza Hezekiya kuti adzafa. Hezekiya atamva zimenezi, anacondelela Yehova kuti am’cilitse misozi ili mbwe! mbwe! mbwe! Yehova anamumvela cifundo Hezekiya ndipo anamuonjezela zaka zina 15. (2 Maf. 20:​1, 5, 6) Zocitika ziwilizi zionetsa bwino lomwe kuti kudzicepetsa kumasonkhezela Yehova kukhala wacifundo ndi wololela.

8. N’zitsanzo ziti zimene zionetsa kuti Yesu ndi wololela? (Maliko 3:​1-6)

8 Kodi Yesu anatengela bwanji citsanzo ca Atate wake? Pamene Yesu anali padziko lapansi, anali kuyesetsa kuthandiza anthu nthawi zonse pakakhala pofunikila. Mwacitsanzo, anacilitsa munthu pa Sabata ngakhale kuti atsogoleli acipemphedzo ouma mtima anali kum’tsutsa. (Welengani Maliko 3:​1-6.) Tsopano, Yesu ndi mutu wa mpingo ndipo amacitabe zinthu mololela. Mwacitsanzo, ngati wina mumpingo wacita cimo lalikulu, iye amamulezela mtima mwa kum’patsa nthawi yoti asinthe zocita zake.​—Chiv. 2:​2-5.

9. Kodi tingaonetse bwanji kuti ndife ololela mwa zimene timaganiza ndi kucita? (Onaninso zithunzi.)

9 Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yehova? Tiyenela kutengela citsanzo ca Yehova mwa kukhala ololela m’zocita ndi zoganiza zathu. (Yak. 3:17) Mwacitsanzo, makolo ololela sayembekezela ana ao kucita zinthu zimene sangakwanitse pa msinkhu wao. Yakobo ndi citsanzo cabwino pa nkhaniyi monga lionetsela lemba la Genesis 33:​12-14. Makolo omwe ndi odzicepetsa komanso ololela ayenela kupewa kuyelekezela mwana wina ndi mnzake. Naonso akulu ayenela kukhala ololela. Angaonetse kulolela pa mamiting’i ao. Mwacitsanzo, mkulu sayenela kuumilila maganizo ake. Koma ayenela kutsatila zimene akulu anzake agwilizana malinga ngati sizisemphana ndi mfundo za m’Baibo. (1 Tim. 3:​2, 3) Tonsefe tiyenela kumvetsa mmene ena akuonela zinthu komanso mmene akumvela, ngakhale pomwe tikuona zinthu mosiyana. (Aroma 14:1) Aliyense mumpingo ayenela kucita zonse zimene angathe kuti “anthu onse adziwe kuti ndi [wololela].”​—Afil. 4:5.

Zithunzi: Tate akusangalala pamene akulalikila ku nyumba ndi nyumba ndi ana ake. 1. Akumwetulila pamene mwana wake wamwamuna akugawila bulosha yakuti “Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!”. 2. Pambuyo pake, akumwetulilanso pamene mwana wake wamkazi akugawila kakhadi kopemphela phunzilo la Baibo.

Tateyu waonetsa kuti ndi wololela mwa kusayelekezela zimene ana ake acita (Onani ndime 9)


YEHOVA NDI WOLEZA MTIMA

10. Kodi Yehova waonetsa motani kuti ndi woleza mtima?

10 Mwacionekele, inunso mungabvomeleze kuti anthu onyada sakonda kuwayembekezetsa. Kunyada kumawapangitsa kukhala osaleza mtima. Izi n’zosiyana kwambili ndi mmene Yehova alili! Iye ndiye cimake ca khalidwe la kuleza mtima. Mwacitsanzo, m’masiku a Nowa, Yehova anati adzayembekezela zaka 120 asanaononge oipa. (Gen. 6:3) Izi zinapatsa Nowa nthawi yoti alele ana ndi kumanga cingalawa limodzi ndi banja lake. Komanso pa nthawi ina, mngelo amene anali kuimilako Yehova anamvetsela Abulahamu moleza mtima, pamene anali kufunsa mafunso okhudza kuonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora. Munthu wonyada akananena kuti, ‘Kodi ukuganiza kuti sindikudziwa zimene ndikucita?’ Koma potengela Yehova, mngeloyo analeza naye mtima Abulahamu.​—Gen. 18:​20-33.

11. Malinga ndi lemba la 2 Petulo 3:​9, n’cifukwa ciani Yehova akuleza mtima masiku ano?

11 Yehova akulezabe mtima mpaka pano. Akuyembekezela nthawi imene anaika kuti aononge dzikoli. Cifukwa ciani? “Cifukwa sakufuna kuti munthu aliyense adzaonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.” (Welengani 2 Petulo 3:9.) Kodi kuleza mtima kwa Yehova kwapita pacabe? Kutali-tali! M’malomwake, kwapatsa anthu mamiliyoni ambili mwai wakuti akhale mabwenzi ake. Ndipo tikuyembekezela kuti anthu enanso mamiliyoni ambili acita cimodzi-modzi. Ngakhale n’telo, kuleza mtima kwa Yehova kuli ndi malile. Yehova amakonda anthu koma salekelela zoipa. Iye sadzalola anthu oipa kupitiliza kukhala padzikoli.​—Hab. 2:3.

12. Kodi Yesu akutengela bwanji citsanzo ca Yehova pa nkhani ya kuleza mtima?

12 Kodi Yesu anatengela bwanji citsanzo ca Atate wake? Yesu wakhala akutengela kuleza mtima kwa Atate wake kwa zaka masauzande. Wakhala akuona Satana akuneneza Yehova ndi anthu okhulupilika. (Gen. 3:​4, 5; Yobu 1:11; Chiv. 12:10) Yesu wakhala akuonanso mabvuto osaneneka. Mosakaika konse, iye akucita kulaka-laka “kuti aononge nchito za Mdyelekezi”! (1 Yoh. 3:8) Kodi n’ciani cathandiza Yesu kuyembekezela moleza mtima mpaka pamene Yehova adzamuuza kuti nthawi yakwana yakuti aononge nchito za Mdyelekezi kothelatu? Cimodzi cimene cam’thandiza ndi kudzicepetsa. Akudziwa kuti ndi udindo wa Yehova kusankha nthawi yoononga dziko loipali.​—Mac. 1:7.

13. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anali woleza mtima pocita zinthu ndi ophunzila ake? Nanga n’cifukwa ciani anali kuwalezela mtima?

13 Yesu anali kucitanso zinthu moleza mtima ndi atumwi ake. Mwacitsanzo, ngakhale kuti ophunzila ake anali kukangana mobweleza-bweleza pa nkhani yakuti wamkulu ndani, iye sanawaone ngati olephela. Anawalezelabe mtima. (Luka 9:46; 22:​24-27) Anali ndi cikhulupililo cakuti adzasintha m’kupita kwa nthawi. Kodi inu munacitapo colakwa cimodzi-modzi mobweleza-bweleza? Ngati n’telo, kodi sindinu woyamikila kukhala ndi Mfumu yodzicepetsa komanso yoleza mtima imeneyi?

14. Kodi tingatani kuti tikhale oleza mtima?

14 Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yehova? Kuti tiziganiza ndi kucita zinthu ngati Yehova, coyamba tiyenela kuphunzila kuganiza ngati Khristu. (1 Akor. 2:16) N’ciani cingatithandize kudziwa bwino maganizo a Yesu? Cimodzi cofunika kwambili ndi kuwelenga nkhani za m’Baibo zofotokoza umoyo wa Yesu. Kenako tiyenela kupatula nthawi yoganizila zimene Yesu anacita, komanso cifukwa cimene anacitila zimenezo. Ndipo tisalephele kupemphela kwa Yehova kuti atithandize kutengela maganizo a Yesu. Tikamayesetsa kutengela maganizo a Khristu, cidzakhala cosabvuta kutengela kuleza mtima kwa Yehova. Tikatelo, tidzatha kulezela mtima anthu ena ndi kudzilezela mtima ife eni.​—Mat. 18:​26-30, 35.

YEHOVA AMALEMEKEZA ANTHU ODZICEPETSA

15. Fotokozani zitsanzo zoonetsa kuti Yehova amawakonda anthu odzicepetsa. (Salimo 138:6)

15 Welengani Salimo 138:6. N’zocititsa cidwi kwambili kuti Yehova, amene ndi wapamwamba zedi kuposa wina aliyense m’cilengedwe conse, amaganizila anthu odzicepetsa. Tiyeni tioneko zitsanzo zocepa cabe za anthu otsika amene Yehova anawalemekeza. Ena mwa iwo angakhale oti sitiwadziwa bwino. Koma mbili yao imapezeka m’Baibo. Mwacitsanzo, Yehova anauzila Mose kulemba za mlezi wina dzina lake Debora. Mleziyu anatumikila kwa zaka ngati 125 m’banja la Isaki ndi la Yakobo! Ngakhale kuti sitidziwa zambili za mzimai wokhulupilikayu, Yehova anaonetsetsa kuti m’Mau ake mwalembedwa mfundo yoonetsa kuti anthu anali kum’konda kwambili. (Gen. 24:59; 35:​8, mau a m’munsi.) Komanso patapita zaka mahandiledi, Yehova anakweza Davide, yemwe anali m’busa, mwa kumuika kukhala mfumu ya mtundu wa Aisiraeli. (2 Sam. 22:​1, 36) Ndipo Yesu atabadwa, Yehova anatumiza angelo kuti akalengeze kwa abusa zakuti Mesiya wabadwa mumzinda wapafupi wa Betelehemu. Uwu unali mwai wapadela cifukwa abusawo ndiwo anali oyamba kudziwa kuti Mesiya wabadwa. (Luka 2:​8-11) Ndiponso pamene Yosefe ndi Mariya anapita ndi Yesu ku kacisi, Yehova analemekeza Simiyoni ndi Ana, omwe anali acikulile, mwa kuwapatsa mwai woona mwana wake. (Luka 2:​25-30, 36-38) Kunena zoona, “ngakhale kuti Yehova ali pamwamba, amaona wodzicepetsa”!

16. Kodi Yesu anatengela bwanji citsanzo ca Atate wake pa nkhani ya kulemekeza anthu odzicepetsa?

16 Kodi Yesu anatengela bwanji citsanzo ca Atate wake? Mofanana ndi Atate wake, Yesu anali kuwalemekeza anthu odzicepetsa. Iye anaphunzitsa anthu “osaphunzila ndiponso anthu wamba” coonadi conena za Ufumu wa Mulungu. (Mac. 4:13; Mat. 11:25) Yesu anali kucilitsanso odwala, ndipo anali kutelo m’njila yowapatsa ulemu. (Luka 5:13) Usiku woti Yesu aphedwa mawa lake, anasambika mapazi a atumwi ake, imene inali nchito ya kapolo. (Yoh. 13:5) Ndipo atatsala pang’ono kubwelela kumwamba, Yesu analemekeza ophunzila ake onse, kuphatikizapo ife, mwa kutisiyila nchito yofunika koposa yothandiza anthu kukapeza moyo wosatha.​—Mat. 28:​19, 20.

17. Kodi tingawalemekeze bwanji anthu ena? (Onaninso cithunzi.)

17 Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yehova? Timalemekeza ena tikamawauzako uthenga wabwino mosasamala kanthu za mmene anakulila, khungu lao kapena maphunzilo ao. Ndipo timalemekeza abale ndi alongo athu mwa kuwaona kuti ndi otiposa, mosasamala kanthu za maluso kapena udindo umene tingakhale nao. (Afil. 2:3) Yehova amasangalala tikakhala patsogolo pa nkhani yoonetsana ulemu m’njila zimene tachulazi komanso zina.​—Aroma 12:10; Zef. 3:12.

Alongo awili akuphunzila Baibo ndi mai amene ali mndende.

Timatengela kudzicepetsa kwa Yehova tikamagawilako uthenga wabwino kwa anthu onse (Onani ndime 17)a


18. N’cifukwa ciani mufuna kutengela kudzicepetsa kwa Yehova?

18 Tikamayesetsa kutengela Atate wathu wacikondi wakumwamba, tidzakhala ofikilika kwambili, ololela kwambili, komanso oleza mtima kwambili. Ndipo tidzalemekeza ena monga mmene Yehova amacitila. Tisaiwale, tikacita zonse zotheka kuti titengele citsanzo ca Mulungu wathu wodzicepetsa, tidzakhala amtengo wapatali zedi pamaso pake!​—Yes. 43:4.

KODI KUDZICEPETSA KUNGAKUTHANDIZENI BWANJI KUKHALA . . .

  • wofikilika?

  • wololela?

  • woleza mtima?

NYIMBO 159 M’patseni Ulemelelo Yehova

a MAU OFOTOKOZELA ZINTHUNZI: Alongo akutengela citsanzo ca Yehova ca kudzicepetsa mwa kuphunzitsa anthu omwe ali m’ndende.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani