Maulaliki Acitsanzo
Kuyambitsa Maphunzilo a Baibulo pa Ciŵelu Coyamba mu June
“Tikuceza ndi anzathu pokambilana nao funso locititsa cidwi ili.” [Onetsani funso loyamba limene lili pacikuto ca kumapeto kwa Nsanja ya Mlonda ya June 1.] Kodi muganiza bwanji?” Yembekezani ayankhe. Ndiyeno kambilanani mfundo zimene zili pansi pa funso loyamba ndi kuŵelenga naye lemba limodzi limene silinagwidwe mau. Kenako mugaŵileni magazini, ndi kupanga makonzedwe akuti mudzakambitsilanenso funso lotsatila.
Nsanja ya Mlonda June 1
“Kusuta fodya kumapha anthu pafupifupi 6,000,000 pa caka. Muganiza kuti n’ciani cimene cingacepetse vuto limeneli? [Yembekezani ayankhe.] Ambili athandizidwa kusiya kapena kupewa kusuta fodya poganizila mmene Mulungu amaonela nkhani imeneyi. Mwacitsanzo, vesi ili la m’Baibulo lapangitsa anthu ena kuganizila mmene kusuta fodya kumakhudzila ena. [Ŵelengani 1 Akorinto 10:24.] Magazini iyi ikufotokoza mmene kuganizila za mmene Mulungu amaonela kusuta fodya kungathandizile munthu kusiya kusuta.”
Galamukani! May
“Intaneti yapangitsa anthu kukhala ndi mabwenzi ambili kuposa kale. Kodi munganene kuti ndi khalidwe labwino kwambili liti limene bwenzi labwino liyenela kukhala nalo? [Yembekezani ayankhe.] Naci citsanzo cothandiza pankhani ya mabwenzi cimene cili m’Baibulo. [Ŵelengani Yakobo 1:19.] Magazini iyi ikufotokoza mfundo zinai zimene zingatithandize kukhala munthu amene ena angakonde kukhala bwenzi lao.”