Maulaliki Acitsanzo
Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo pa Ciŵelu Coyamba mu June
“Pafupi-fupi munthu aliyense amene timakamba naye amafuna kuti padziko pakhale mtendele. Koma nkhondo ziliko. M’kuona kwanu, n’cifukwa ciani mtendele uoneka kukhala wosatheka?” Yembekezani ayankhe. Ndiyeno muonetseni nkhani ili patsamba lothela kucikuto kwa Nsanja ya Olonda ya June 1, ndi kukambilana naye nkhani ili pansi pa funso loyamba ndipo ŵelengani naye lemba ngakhale limodzi pa malembawo. Kenako m’gaŵileni magazini ndi kupangana kuti mukabwelenso kudzakambilana naye funso lotsatila.
Cidziŵitso: Citsanzo ici ciyenela kucitika pa kukumana kokonzekela ulaliki pa June 1.
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova June 1
“Tikucezela anansi athu mwacidule m’dela lino ponena za vuto limene anthu ambili amakumana nalo. Anthu ambili acitilidwapo tsankho panthawi ina yake. M’kuona kwanu kodi pali dziko limene kulibe tsankho? [Yembekezani kuti ayankhe.] Onani mmene Mulungu amaonela anthu onse. [Ŵelengani Machitidwe 10:34.] Magazini iyi ifotokoza mmene Mulungu adzathetsela tsankho.”
Galamukani! June
“Tifuna kumvako malingalilo anu pa nkhani ina yake.” Mwacibadwa ife tonse timafuna umoyo wabwino. Kodi muganiza kuti umoyo wabwino tingaupeze mwa kugula katundu wambili? [Yembekezani kuti ayankhe.] Onani mau amphamvu a Yesu awa. [Ŵelengani Luka 12:15.] Magazini iyi ifotokoza mmene tiyenela kuonela zinthu za kuthupi ndipo ipeleka mfundo zothandiza za mmene tiyenela kugwilitsila nchito bwino ndalama.”