Kodi Mukukumbukila?
Kodi munaŵelenga mosamala magazini a caka cino a Nsanja ya Mlonda? Yesani kuyankha mafunso otsatilawa:
Kodi tingapindule bwanji tikamalankhula na Yehova, kumumvetsela, na kusinkha-sinkha za iye?
Tidzayamba kupanga zisankho zabwino, tidzakhala aphunzitsi abwino, cikhulupililo cathu cidzalimbilako, komanso cikondi cathu pa Yehova cidzakula.—w22.01, mas. 30-31.
Kodi tingapindule bwanji tikaphunzila kukhulupilila Yehova na anthu omuimila?
Ino ndiyo nthawi yophunzila kukhulupilila kacitidwe ka Mulungu ka zinthu, mwa kusazengeleza kutsatila citsogozo na zigamulo za akulu. Cisautso cacikulu cikadzayamba, tidzakhala okonzeka kutsatila malangizo amene angadzaoneke acilendo kapena ovuta kuwatsatila.—w22.02, mas. 4-6.
Kodi mngelo anafuna kumveketsa mfundo yanji pouza Zekariya za “cingwe ca mmisili womanga nyumba m’dzanja la [Bwanamkubwa] Zerubabele”? (Zek. 4:8-10)
Masomphenya amenewa anatsimikizila anthu a Mulungu kuti ngakhale kuti kacisi sadzakhala waulemelelo monga wa poyamba, adzamalizidwa kumangidwa, ndipo adzakhala mmene Yehova anali kufunila.—w22.03, mas. 16-17.
Kodi tingakhale bwanji “citsanzo . . . m’kalankhulidwe”? (1 Tim. 4:12)
Mwa kukamba mokoma mtima komanso mwaulemu mu ulaliki, kuimba mocokela pansi pamtima, kuyankhapo kaŵili-kaŵili pa misonkhano, kukamba zoona nthawi zonse, kukamba mawu olimbikitsa ena, komanso kupewa kukamba mawu acipongwe.—w22.04, mas. 6-9.
N’cifukwa ciyani cilombo cimodzi cofotokozedwa pa Chivumbulutso 13:1, 2 cili na maonekedwe a zilombo zonse zinayi (maufumu) zochulidwa mu Danieli caputala 7?
Cilombo cofotokozedwa mu Chivumbulutso 13 siciimila ufumu umodzi, monga ufumu wa Roma ayi. Koma cikuimila maboma onse andale amene akhala akulamulila anthu kuyambila kale-kale.—w22.05, tsa. 9.
Kodi ni njila yaikulu iti imene tingaonetsele kuti timakhulupilila cilungamo ca Yehova?
Munthu akatinyoza, kutikhumudwitsa, kapena akatilakwila, timayesetsa kusakwiya kapena kusasunga cakukhosi, na kusiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. Iye adzathetsa mavuto onse obwela kaamba ka ucimo.—w22.06, mas. 10-11.
Kodi m’bale wopeleka pemphelo pa msonkhano ayenela kukumbukila ciyani?
M’pemphelo simopelekela uphungu ku mpingo kapena kupelekelamo zilengezo. Makamaka kuciyambi kwa msonkhano, m’bale wopeleka pemphelo sayenela kukamba “mawu ambili-mbili.” (Mat. 6:7)—w22.07, mas. 24-25.
Kodi “amene anali kucita zoipa adzauka kuti aweluzidwe” mlingalilo lotani? (Yoh. 5:29)
Iwo sadzalandila ciweluzo copeleka cilango, poona zimene anacita asanamwalile. Koma umoyo wawo udzaunikidwa poyang’ana zocita zawo na kaimidwe ka maganizo awo pambuyo poukitsidwa.—w22.09, tsa. 18.
Kodi M’bale J. F. Rutherford anapeleka cilimbikitso cotani pa msonkhano waukulu umene unacitika mu September 1922?
Pa msonkhano waukulu mu mzinda wa Cedar Point, Ohio, ku America, anakamba mokweza kuti: “Onani, Mfumu yayamba kale kulamulila ndipo inu ndinu atumiki ake olengeza ufumuwo. Conco lengezani, lengezani, lengezani Mfumu ndi Ufumu wake!”—w22.10, mas. 3-5.
Kodi Yesaya caputala 30 imaonetsa njila zitatu ziti zimene Mulungu amatithandizila kupilila?
Caputalaci cionetsa kuti (1) iye amamvetsela mapemphelo athu mwachelu na kuwayankha, (2) amatitsogolela, komanso (3) amatidalitsa palipano, na kutilonjeza madalitso ena m’tsogolo.—w22.11, tsa. 9.
N’cifukwa ciyani tingati mawu a pa Salimo 37:10, 11, 29 anakwanilitsidwa kalelo ndipo adzakwanilitsidwanso kutsogolo?
Mawu a Davide amenewa afotokoza bwino mmene zinthu zinalili bwino mu Isiraeli, monga panthawi ya ulamulilo wa Solomo. Yesu pokamba za madalitso a kutsogolo m’paradaiso, anagwila mawu a mu vesi 11. (Mat. 5:5; Luka 23:43)—w22.12, mas. 8-10, 14.