LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
Cilengezo
Taikaponso citundu cina: Mbum
  • Lelo

Ciŵili, July 29

Umandisangalatsa kwambili.​—Luka 3:22.

N’zolimbikitsa zedi kudziŵa kuti Yehova amakonda gulu lonse la anthu ake! Baibo imati: “Yehova amasangalala ndi anthu ake.” (Sal. 149:4) Komabe, nthawi zina ena amalefuka moti amafika podzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova amakondwela nane?’ Ena mwa alambili okhulupilika a Yehova ochulidwa m’Baibo anavutikapo na maganizo otelo. (1 Sam. 1:6-10; Yobu 29:2, 4; Sal. 51:11) Baibo imakamba momveka bwino kuti anthu opanda ungwilo angapeze ciyanjo ca Yehova. Motani? Mwa kukhulupilila Yesu Khristu na kubatizika. (Yoh. 3:16) Mwa kutelo, timaonetsa poyela kuti tinalapa macimo athu, komanso kuti tinapanga lonjezo kwa Mulungu lakuti tidzacita cifunilo cake. (Mac. 2:38; 3:19) Yehova amakondwela ngati tapanga masitepe amenewa kuti tikhale naye pa ubale. Kuwonjezela apo, amakondwela nafe ngati tipitiliza kucita zonse zimene tingathe posunga lumbilo lathu la kudzipatulila. Ndipo amationa kukhala mabwenzi ake a pamtima.​—Sal. 25:14. w24.03 26 ¶1-2

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Citatu, July 30

Sitingasiye kulankhula za zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.​—Mac. 4:20.

Tingatengele citsanzo ca ophunzila mwa kupitiliza kulalikila ngakhale pamene maboma atilamula kuti tileke kulalikila. Tili na cidalilo kuti Yehova adzatithandiza kukwanilitsa utumiki wathu. Conco mupemphani kuti akuthandizeni kukhala wolimba mtima, akupatseni nzelu komanso kuti akuthandizeni kuthana na mavuto. Ambili a ife tikulimbana na mavuto monga matenda, kupsinjika maganizo, kutaikilidwa wokondedwa wathu mu imfa, mavuto a m’banja, mazunzo, kapena vuto lina. Ndipo zinthu monga milili na nkhondo, zapangitsa kuti cikhale covuta kwambili kuthana na mavuto ngati amenewa. Conco, m’khuthulileni za kumtima kwanu Yehova. Muuzeni za vuto lanu mmene mungauzile bwenzi lanu lapamtima. Khalani wotsimikiza kuti Yehova “adzakuthandizani.” (Sal. 37:3, 5) Kulimbikila kupemphela kudzatithandiza ‘kupilila mavuto.’ (Aroma 12:12) Yehova amadziŵa mavuto amene atumiki ake amakumana nawo, “amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.”​—Sal. 145:18, 19. w23.05 5-6 ¶12-15

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Cinayi, July 31

Nthawi zonse muzitsimikizila kuti covomelezeka kwa Ambuye nʼciti.​—Aef. 5:10.

Tikafunika kupanga cisankho cofunika kwambili, tiyenela “kuzindikila cifunilo ca Yehova,” na kucita zinthu mogwilizana na cifuniloco. (Aef. 5:17) Tikamafufuza na kupeza mfundo za m’Baibo zothandiza pa cisankho cimene tifuna kupanga, kwenikweni timakhala tikufunafuna maganizo a Mulungu pa nkhaniyo. Ndipo tikagwilitsa nchito mfundo zake, timapanga zisankho zabwino. Mdani wathu Satana, “Woipayo,” amafuna kuticenjeneka na kufuna-funa zinthu za m’dzikoli n’colinga cakuti tizisoŵelatu nthawi yotumikila Mulungu. (1 Yoh. 5:19) Cingakhale capafupi kwa Mkhristu kutsogoza zakuthupi, maphunzilo, kapena nchito m’malo moseŵenzetsa mipata imene ilipo yotumikila Yehova. Zotelezi zikacitika, zingaonetse kuti munthu wayamba kuyendela maganizo a m’dzikoli. N’zoona kuti zinthu zimenezi si zoipa kwenikweni. Koma si ndiye zomwe tiyenela kutsogoza pa umoyo wathu. w24.03 24 ¶16-17

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani