LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w23 May masa. 2-7
  • Kuwongolela Mapemphelo Athu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kuwongolela Mapemphelo Athu
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • YESU ANALI KUPATULA NTHAWI YOPEMPHELA
  • ZINTHU ZISANU ZIMENE TINGAPEMPHELELE
  • Tiziyamikila Mwayi Wathu wa Pemphelo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Yandikilani kwa Mulungu Kupitila M’pemphelo
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Mwayi Wa Pemphelo
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Muyandikileni Mulungu Kupitila m’Pemphelo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
w23 May masa. 2-7

NKHANI YOPHUNZILA 20

Kuwongolela Mapemphelo Athu

“Mukhuthulileni za mumtima mwanu.”—SAL. 62:8.

NYIMBO 45 Kusinkhasinkha kwa Mtima Wanga

ZIMENE TIKAMBILANEa

Zithunzi: M’bale akupemphela pa nthawi zosiyanasiyana pa tsiku. 1. Atangouka. 2. Asanadye cakudya na banja lake. 3. Asanayambe ulaliki kupitila pa vidiyo. 4. Ali kunja kumalo abata. 5. Asanagone.

Tingam’fikile Yehova m’pemphelo nthawi zonse, na kum’pempha citsogozo pa mbali zonse za umoyo wathu (Onani ndime 1)

1. Kodi Yehova akupempha alambili ake kucita ciyani? (Onaninso cithunzi.)

KODI tingatembenukile kwa ndani tikafuna citonthozo komanso citsogozo? Yankho n’lodziŵikilatu. Tingafikile Yehova Mulungu m’pemphelo. Ndipo n’zimene iye amatipempha kucita. Amafuna kuti tizipemphela kaŵilikaŵili, ‘tizipemphela mosalekeza.’ (1 Ates. 5:17) Tingapemphele kwa iye momasuka, na kum’pempha citsogozo pa mbali zonse za umoyo wathu. (Miy. 3: 5, 6) Pokhala Mulungu wowolowa manja, Yehova sanaike malile kuti tizipemphela kangati kwa iye.

2. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

2 Timauyamikila mwayi wa pemphelo. Koma cifukwa timakhala na zocita zambili, cingativute kupeza nthawi yopemphela. Tingaonenso kuti m’pofunika kuwongolelako mapemphelo athu. Ndife oyamikila kuti timapeza cilimbikitso na citsogozo m’Malemba. M’nkhani ino tikambilane zimene tingacite kuti tizipatula nthawi yopemphela, potengela citsanzo ca Yesu. Tikambilanenso zinthu zofunika zisanu zimene tingachule m’mapemphelo athu kuti akhale abwino koposa.

YESU ANALI KUPATULA NTHAWI YOPEMPHELA

3. Kodi Yesu anali kudziŵa ciyani za pemphelo?

3 Yesu anadziŵa kuti mapemphelo athu ni ofunika kwa Yehova. Asanabwele pa dziko lapansi, iye anaona mmene Atate wake anali kuyankhila mapemphelo a atumiki ake okhulupilika. Mwacitsanzo, pamene Mulungu anali kuyankha mapemphelo ocokela pansi pa mtima a Hana, Davide, Eliya komanso atumiki ena ambili, Yesu anali pambali pake. (1 Sam. 1:10, 11, 20; 1 Maf. 19:4-6; Sal. 32:5) Ndiye cifukwa cake iye anaphunzitsa ophunzila ake kupemphela kaŵilikaŵili komanso mwacidalilo.—Mat. 7:7-11.

4. Kodi mapemphelo a Yesu atiphunzitsa ciyani?

4 Mwa mapemphelo ake kwa Yehova, Yesu anapeleka citsanzo kwa ophunzila ake. Pa utumiki wake wonse, iye anali kupemphela kaŵilikaŵili. Kambili, anali kukhala pakati pa anthu, ndipo anali kukhala wotangwanika. Conco anali kucita kupatula nthawi yoti apemphele. (Maliko 6:31, 45, 46) Iye anali kuuka m’mamaŵa kuti akhale na nthawi yopemphela payekha. (Maliko 1:35) Panthawi ina, anapemphela usiku wonse kuti apange cisankho cofunika kwambili. (Luka 6:12, 13) Panthawi inanso, Yesu anaika maganizo ake pa kukwanilitsa mbali yovuta ya utumiki wake wa padziko lapansi. Conco anapemphela mobweleza-bweleza usiku woti maŵa lake aphedwa.—Mat. 26:39, 42, 44.

5. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu pa nkhani yopemphela?

5 Citsanzo ca Yesu citiphunzitsa kuti ngakhale titangwanike bwanji, tiyenela kupatula nthawi yopemphela. Monga Yesu, tingafunike kucita kuipatula nthawi yopemphela. Mwina tingafunike kuuka m’mawa kwambili, kapena kugona mocedwako usiku kuti tipemphele. Tikatelo, timaonetsa Yehova kuti timayamikila mphatso yapadela imeneyi. Mlongo wina dzina lake Lynne akumbukila mmene anamvela nthawi yoyamba atadziŵa za mwayi wa pemphelo. Iye anati: “N’tadziŵa kuti ningakambe na Yehova nthawi iliyonse, zinanithandiza kumuona kuti ni Bwenzi langa lapamtima, komanso kuti niwongolele mapemphelo anga.” Mosakaikila, ambili a ife timamva conco. Tiyeni tikambilane zinthu zofunika zisanu zimene tingachule m’mapemphelo athu.

ZINTHU ZISANU ZIMENE TINGAPEMPHELELE

6. Malinga na Chivumbulutso 4:10, 11, kodi Yehova ni woyenela kulandila ciyani?

6 Kutamanda Yehova. M’masomphenya ocititsa cidwi, mtumwi Yohane anaona akulu 24 akulambila Yehova kumwamba. Iwo anatamanda Mulungu poona kuti ni woyenela kulandila “ulemelelo ndi ulemu.” (Ŵelengani Chivumbulutso 4:10, 11.) Angelo okhulupilika nawonso ali na zifukwa zambili zotamandila Yehova na kum’lemekeza. Iwo amakhala naye kumwamba, ndipo anafika pom’dziŵa bwino kwambili. Amaona makhalidwe ake mwa zocita zake. Conco, amasonkhezeledwa kum’tamanda.—Yobu 38:4-7.

7. Tingatamande Yehova pa zifukwa ziti?

7 Nafenso tizitamanda Yehova m’mapemphelo athu, mwa kuchula zimene timakonda komanso zimene timayamikila zokhudza iye. Pamene muŵelenga na kuphunzila Baibo, muziyesa kupeza makhalidwe a Yehova amene amakukhudzani mtima. (Yobu 37:23; Aroma 11:33) Kenako, muuzeni Yehova mmene mumamvela za makhalidwe akewo. Tingam’tamandenso cifukwa amatithandiza, komanso amathandiza abale na alongo athu. Iye amatisamalila na kutiteteza nthawi zonse.—1 Sam. 1:27; 2:1, 2.

8. Kodi zina mwa zifukwa zomuyamikila Yehova n’ziti? (1 Atesalonika 5:18)

8 Kuyamika Yehova. Tili na zifukwa zambili zoyamikila Yehova m’pemphelo. (Ŵelengani 1 Atesalonika 5:18.) Tingamuyamikile pa zabwino zonse zimene tili nazo, cifukwa mphatso iliyonse yabwino imacokela kwa iye. (Yak. 1:17) Tingamuyamikile cifukwa cotipatsa dziko lapansi lokongola, na zinthu zacilengedwe zocititsa cidwi. Tingamuyamikilenso potipatsa moyo, banja, mabwenzi, komanso ciyembekezo. Ndipo tingamuyamikilenso potilola kukhala naye pa ubwenzi wamtengo wapatali.

9. N’cifukwa ciyani tiyenela kukulitsa mzimu woyamikila Yehova?

9 Aliyense pacake angafunike kuyesetsa kuti apeze zifukwa zomuyamikila Yehova. Anthu ambili m’dzikoli ni osayamika. Amaika maganizo awo pa zimene akufuna, m’malo moyamikila zimene ali nazo kale. Ngati mzimu umenewu ungatiyambukile, mapemphelo athu angamakhale mndandanda wa zopempha basi. Kuti tipewe zimenezi, tiyenela kupitiliza kukulitsa mzimu woyamikila pa zonse zimene Yehova amaticitila.—Luka 6:45.

Mlongo akupemphela pa mtenje wa nyumba yake usiku. Pa thebulo lili pafupi naye pali Baibo na buku lolembamo manotsi.

Kumuyamikila Yehova pa zimene amaticitila kumatithandiza kupilila (Onani ndime 10)

10. Kodi kukhala woyamikila kunam’thandiza bwanji mlongo wina kupilila? (Onaninso cithunzi.)

10 Mzimu woyamikila ungatithandize kupilila mavuto. Ganizilani cocitika ca mlongo Kyung-sook, copezeka mu Nsanja ya Mlonda ya January 15, 2015. Mlongoyo anamupeza na matenda aakulu a khansa. Iye anati: “N’tauzidwa kuti nili na matendawa, n’nakhumudwa kwambili. N’naona monga zonse zathela pamenepa, ndipo n’nali na mantha kwambili.” N’ciyani cinam’thandiza kupilila? Iye ananena kuti usiku uliwonse asanagone anali kupita pa mtenje wa nyumba yake kukapemphela mokweza, na kuchula zinthu zisanu zimene anali woyamikila pa tsikulo. Kucita izi kunacepetsa nkhawa zake, ndipo kunam’limbikitsa kuonetsa cikondi cake pa Yehova. Mlongoyo anaona mmene Yehova amathandizila atumiki ake okhulupilika akakumana na mavuto. Ndipo anazindikila kuti tili na madalitso ambili kuposa mavuto amene timakumana nawo mu umoyo. Monga Kyung-sook, tili na zifukwa zambili zoyamikila Yehova, ngakhale pamene tikukumana na mayeso. Kumuyamikila m’pemphelo kungatithandize kupilila na kukhalabe osatekeseka.

11. N’cifukwa ciyani ophunzila a Yesu anafunika kulimba mtima Yesu atabwelela kumwamba?

11 Kupempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala wolimba mtima mu ulaliki. Atatsala pang’ono kubwelela kumwamba, Yesu anakumbutsa ophunzila ake za utumiki umene anapatsidwa wocitila umboni za iye “mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” (Mac. 1:8; Luka 24:46-48) Patangopita nthawi yocepa, atsogoleli aciyuda anagwila mtumwi Petulo na Yohane n’kuwapeleka ku Khoti Yapamwamba ya Ayuda. Kumeneko, amuna okhulupilika amenewa analamulidwa kuti aleke kulalikila, ndipo anawaopseza. (Mac. 4:18, 21) Kodi Petulo na Yohane anacita motani?

12. Malinga na Machitidwe 4:29, 31, kodi ophunzila anacita ciyani?

12 Poyankha atsogoleli aciyuda amene anali kuwaopseza, Petulo na Yohane anati: “Weluzani nokha, ngati n’koyenela pamaso pa Mulungu kumvela inu koposa Mulungu. Koma ife sitingaleke kulankhula zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.” (Mac. 4:19, 20) Petulo na Yohane atamasulidwa, ophunzilawo anapemphela kwa Yehova mofuula kuti awathandize kucita cifunilo cake. Iwo anapemphela kuti: “Lolani kuti akapolo anu apitilize kulankhula mawu anu molimba mtima.” Yehova anayankha pemphelo lawo locokela pansi pa mtima.—Ŵelengani Machitidwe 4:29, 31.

13. Tingaphunzile ciyani kwa m’bale Jin-hyuk?

13 Tingatengele citsanzo ca ophunzila mwa kupitiliza kulalikila ngakhale pamene maboma atilamula kuti tileke kulalikila. Ganizilani citsanzo ca m’bale Jin-hyuk, amene anaponyedwa m’ndende cifukwa cokana kuloŵa usilikali. Ku ndendeko, anapatsidwa nchito yosamalila akaidi ena amene anali kukhala m’zipinda za okha. Koma sanali kuloledwa kukambilana nawo nkhani zina, kuphatikizapo za Baibo. Iye anapempha Mulungu kuti am’thandize kulalikila mosamala pa mpata uliwonse komanso kuti akhale wolimba mtima. (Mac. 5:29) Iye anati: “Yehova anayankha mapemphelo anga mwa kunilimbitsa mtima na kunipatsa nzelu, kuti nikhale na maphunzilo a Baibo ambili otsogozedwa mphindi zisanu n’taimilila pa khomo la citolokosi. Ndiyeno usiku n’nali kulemba makalata amene n’nali kupatsa akaidiwo tsiku lotsatila.” Ifenso tili na cidalilo kuti Yehova adzatithandiza kukwanilitsa utumiki wathu. Monga Jin-hyuk, tingapemphe Yehova kuti atithandize kukhala olimba mtima na kutipatsa nzelu.

14. N’ciyani cingatithandize tikakumana na mavuto? (Salimo 37:3, 5)

14 Kum’pempha Yehova kuti akuthandizeni kuthana na mavuto. Ambili a ife tikulimbana na mavuto monga matenda, kupsinjika maganizo, kutaikilidwa wokondedwa wathu mu imfa, mavuto a m’banja, mazunzo, kapena vuto lina. Ndipo zinthu monga milili na nkhondo, zapangitsa kuti cikhale covuta kwambili kuthana na mavuto ngati amenewa. Conco, m’khuthulileni za kumtima kwanu Yehova. Muuzeni za vuto lanu mmene mungauzile bwenzi lanu lapamtima. Khalani wotsimikiza kuti Yehova “adzacitapo kanthu” kuti akuthandizeni.—Ŵelengani Salimo 37:3, 5.

15. Kodi pemphelo ingatithandize bwanji ‘kupilila cisautso’? Fotokozani citsanzo.

15 Kulimbikila kupemphela kudzatithandiza ‘kupilila cisautso.’ (Aroma 12:12) Yehova amadziŵa mavuto amene atumiki ake amakumana nawo, ‘amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.’ (Sal. 145:18, 19) Mpainiya wina wa zaka 29 dzina lake Kristie, anaona kuti mfundo imeneyi ni yoona. Mosayembekezela iye anayamba kudwala matenda aakulu. Izi zinapangitsa kuti ayambe kuvutika maganizo kwambili. Patapita nthawi, amayi ake anadwala matenda osacilitsika. Kristie anati: “N’nali kupemphela kwambili kuti Yehova azinipatsa mphamvu zonithandiza kupilila tsiku lililonse. N’nali kuyesetsa kucita zinthu zauzimu mwa kupezeka pa misonkhano na kucita phunzilo la munthu mwini.” Anapitiliza kuti: “Pemphelo inanithandiza kupilila pa nthawi zovuta zimenezo. N’nali kudziwa kuti Yehova anali nane pa nthawi yonseyo, ndipo maganizo amenewa ananithandiza kupeza citonthozo. Ngakhale kuti matenda anga sanathe nthawi yomweyo, Yehova anayankha mapemphelo anga mwa kunipatsa mtendele wa mumtima.” Tisamaiŵale kuti “Yehova amadziŵa kupulumutsa anthu odzipeleka kwa iye akakhala pa mayeselo.”—2 Pet. 2:9.

Zithunzi: M’bale akucita zinthu zom’thandiza kukaniza mayeselo. 1. Akupemphela mocokela pansi pa mtima. 2. Akucotsa apu ina yake pa tabuleti yake. 3. Akuŵelenga Baibo.

Kuti mukanize mayeselo, (1) pemphani thandizo kwa Yehova, (2) citani mogwilizana na mapemphelo anu, komanso (3) limbitsani ubale wanu na Yehova (Onani ndime 16-17)

16. N’cifukwa ciyani tifunikila thandizo la Yehova kuti tikanize mayeselo?

16 Kupempha Yehova kuti akuthandizeni kukaniza mayeselo. Pokhala anthu opanda ungwilo, nthawi zonse timalimbana na mayeselo ofuna kucita zinthu zoipa. Satana akucita ciliconse cotheka kuti cikhale covuta kwa ife kukaniza mayeselo amenewa. Imodzi mwa njila zimene amagwilitsa nchito pofuna kuwononga kaganizidwe kathu, ni kuonelela zosangalatsa zoipa. Zosangalatsa zimenezo zingapangitse kuti tikhale na maganizo oipa. Ndipo maganizo oipawo angacititse kuti tikhale odetsedwa pamaso pa Yehova, komanso angatitsogolele ku chimo lalikulu.—Maliko 7:21-23; Yak. 1:14, 15.

17. Tikapempha thandizo, kodi tiyenela kucita ciyani kuti tikanize mayeselo? (Onaninso cithunzi.)

17 Tifunikila thandizo la Yehova kuti tikanize mayeselo akuti ticite zoipa. M’pemphelo lake lacitsanzo, Yesu anachula cinanso cimene tingapemphe. Anati: “Musatiloŵetse m’mayeselo, koma mutilanditse kwa woipayo.” (Mat. 6: 13) Yehova afuna kutithandiza, koma tiyenela kum’pempha kuti atithandize. Cina, tiyenela kucita mogwilizana na mapemphelo athu. Tingatelo mwa kuyesetsa kupewa maganizo oipa ofala m’dziko la Satanali. (Sal. 97:10) M’malo mwake, tiyenela kudzaza maganizo athu na zinthu zabwino mwa kuŵelenga Baibo na kuiphunzila. Cina cimene cingateteze maganizo athu, ni kupezeka ku misonkhano komanso kulalikila. Ndipo Yehova analonjeza kuti sadzalola kuti tiyesedwe kufika pamene sitingapilile.—1 Akor. 10:12, 13.

18. Ponena za pemphelo, kodi tonsefe tiyenela kucita ciyani?

18 Kuti tikhalebe okhulupilika kwa Yehova m’masiku ano ovuta, aliyense wa ife ayenela kupemphela kwambili kuposa kale lonse. Conco tizipatula nthawi tsiku lililonse yopemphela mocokela pansi pa mtima. Yehova amafuna kuti tikamapemphela, ‘tizim’khuthulila za mu mtima mwathu.’ (Sal. 62:8) Mtamandeni Yehova na kumuyamikila pa zonse zimene amaticitila. Cina, m’pempheni kuti akulimbitseni mtima mu ulaliki. Cinanso, m’condeleleni kuti akuthandizeni kupilila vuto lililonse komanso kukaniza mayeselo. Conde, musalole ciliconse kapena aliyense kukuletsani kupemphela kwa Yehova nthawi zonse. Nanga kodi Yehova amayankha motani mapemphelo athu? Funso lofunika limeneli lidzayankhidwa m’nkhani yotsatila.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti pemphelo n’lofunika kwambili kwa iye?

  • Kodi zina mwa zinthu zimene tingachule m’mapemphelo athu n’ziti?

  • Kodi mudzayesetsa kucita ciyani pa nkhani yopemphela?

NYIMBO 42 Pemphelo la Mtumiki wa Mulungu

a Timafuna kuti mapemphelo athu azikhala ngati makalata ocokela pansi pa mtima opita kwa bwenzi lathu lokondeka. Ngakhale n’telo, nthawi zina cimakhala covuta kupatula nthawi yopemphela. Cingakhalenso covuta kudziŵa zimene tingachule m’pemphelo. M’nkhani ino, tikambilane mbali ziŵili zofunika zimenezi.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani