LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 3/1 masa. 3-6
  • Zimene Mulungu Wakucitilani

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Zimene Mulungu Wakucitilani
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • “MULUNGU ANAKONDA KWAMBILI DZIKO”
  • “ANAPELEKA MWANA WAKE WOBADWA YEKHA”
  • “ALIYENSE WOKHULUPILILA IYE”
  • “ASAONONGEKE, KOMA AKHALE NDI MOYO WOSATHA”
  • MULUNGU WAKUCITILANI ZAMBILI
  • N’cifukwa Ciani Yesu Anavutika Ndi Kutifela?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Kodi Imfa ya Yesu Ingatipulumutse Bwanji?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Ni Mphatso Iti Yoposa Zonse?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Kodi Yesu Kristu Ndani?
    Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 3/1 masa. 3-6

Nkhani Ya Pacikuto

Zimene Mulungu Wakucitilani

“Pakuti Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asaonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yohane. 3:16.

Limeneli ndi limodzi mwa mavesi odziŵika kwambili ndiponso limene anthu nthawi zambili amagwila mau m’Baibulo. Ena amati palibe vesi lina limene limafotokoza mwacidule ndi momveka bwino cikondi ca Mulungu pa anthu ndi njila yowapulumutsila. Cifukwa ca zimenezi, m’maiko ena lemba la Yohane 3:16 kapena mau ake, nthawi zambili amalembedwa pa zocitika zosiyana-siyana, pa zomata pa magalimoto, ndi pa zinthu zosiyana-siyana.

Kaya akhale ndi zolinga zotani, anthu amene amalemba lembali amakhulupilila kuti cikondi ca Mulungu cidzacititsa kuti akakhale kwamuyaya. Bwanji ponena za inuyo? Kodi mungapindule bwanji ndi cikondi ca Mulungu? Kodi muganiza n’ciani cimene Mulungu wacita cimene cionetsa kuti amakukondani?

“MULUNGU ANAKONDA KWAMBILI DZIKO”

Anthu ambili amam’lemekeza Mulungu cifukwa cakuti analenga zinthu zakuthambo, za padziko lapansi, ndi anthu. Zamoyo zinalengedwa m’njila yabwino ndi yocititsa cidwi, ndipo zimenezi zionetsa kuti Mlengi wake ndi wanzelu kwambili. Anthu ambili masiku onse amayamikila Mulungu cifukwa ca mphatso ya moyo. Iwo amazindikilanso mfundo yakuti, kuti apitilize kukhala ndi moyo ndi kusangalala amadalila Mulungu kuti awapatse zinthu zonse zocilikiza moyo monga cakudya, mpweya ndi madzi.

Tifunika kumuyamikila Mulungu kaamba ka zinthu zonsezi. Iye ndi Mlengi wathu ndipo amatisamalila. (Salimo 104:10-28; 145:15, 16; Machitidwe 4:24) Timayamikila cikondi cimene Mulungu amatisonyeza tikaganizila zonse zimene amaticitila kuti tikhale ndi moyo. Mtumwi Paulo anati: “[Mulungu] amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse. Pakuti cifukwa ca iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.”—Machitidwe 17:25, 28.

Mulungu amaonetsa cikondi cake m’njila zambili osati cabe kutisamalila mwakuthupi. Iye anatilenganso mwapadela ndipo watilemekeza mwa kutipatsa mtima wofuna kumulambila, ndipo amatithandiza kucita zimenezi. (Mateyu 5:3) Kaamba ka zimenezi, anthu omvela angathe kukhala mbali ya banja la Mulungu, “ana” ake.—Aroma 8:19-21.

Lemba la Yohane 3:16 limanenanso kuti Mulungu anaonetsa cikondi cake mwa kutumiza Yesu, Mwana wake, padziko lapansi kuti adzatiphunzitse za Mulungu, Atate ake, ndi kudzatifela. Koma ngakhale n’conco, anthu ambili samvetsetsa cifukwa cake Yesu anafela mtundu wa anthu ndi mmene imfa yake ilili umboni wakuti Mulungu amatikonda. Tiyeni tione mmene Baibulo limafotokozela cifukwa cake Yesu anafa ndiponso phindu la imfa yake.

“ANAPELEKA MWANA WAKE WOBADWA YEKHA”

Anthu onse amadwala, amakalamba ndi kufa. Koma ici sicinali cifuno ca Mulungu poyamba. Iye anapatsa anthu oyambilila ciyembekezo cokhala ndi moyo kosatha m’paladaiso padziko lapansi. Koma anthuwo anafunika kucita cina cake kuti akhalebe ndi moyo. Anafunika kumvela Mulungu. Mulungu anakamba kuti ngati anthuwo sadzamumvela, adzafa. (Genesis 2:17) Koma munthu woyamba anapandukila ulamulilo wa Mulungu, ndipo anabweletsa imfa pa iye ndi ana ake. Mtumwi Paulo anakamba kuti ‘ucimo unaloŵa m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa ucimo, ndipo imfayo inafalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa.’—Aroma 5:12.

Mulungu “amakonda cilungamo.” (Salimo 37:28) Ngakhale kuti Mulungu sanalekelele cimo la dala la munthu woyamba, iye sanaweluze kuti anthu onse apitilize kuvutika ndi kufa cifukwa ca kusamvela kwa munthu mmodzi. Komabe, mwa kugwilitsila nchito lamulo lakuti “moyo kulipila moyo,” Mulungu anaonetsa cilungamo ndi kucititsa kuti anthu omvela akhalenso ndi ciyembekezo ca moyo wosatha. (Ekisodo 21:23) Koma funso ndi lakuti, Kodi zikanatheka bwanji kuti moyo wangwilo umene Adamu anataya uomboledwe? Yankho: Panafunika wina kuti apeleke nsembe moyo wangwilo wofanana ndi umene Adamu anali nao.

Mwacionekele, palibe mbadwa yopanda ungwilo ya Adamu imene ikanatha kupeleka nsembe imeneyo. Yesu yekha ndi amene akanatha kucita zimenezi. (Salimo 49:6-9) Popeza kuti Yesu sanatengele ucimo ulionse, iye anali wangwilo mofanana ndi Adamu. Conco mwa kupeleka moyo wake monga nsembe, Yesu anaombola anthu ku ukapolo wa ucimo. Mwa kucita zimenezi, iye anapatsa mbadwa za banja loyamba mwai wosangalala ndi moyo wangwilo wofanana ndi umene Adamu ndi Hava anali nao. (Aroma 3:23, 24; 6:23) Kodi tingacite ciani kuti tipindule ndi cikondi cacikulu cimeneci?

“ALIYENSE WOKHULUPILILA IYE”

Tikaonanso, lemba la Yohane 3:16 lili ndi mau akuti “aliyense wokhulupilila [Yesu] asaonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” Zimenezi zitanthauza kuti tifunika kucitapo kanthu kuti tilandile mphatso ya moyo wosatha. Tiyenela kukhulupilila Yesu ndi kumumvela kuti ‘tikakhale ndi moyo wosatha.’

Mwina mungadzifunse kuti: ‘N’cifukwa ciani kumvela n’kofunikanso? Kodi Yesu sanakambe kuti “aliyense wokhulupilila iye” adzakhala ndi moyo wosatha?’ N’zoona kuti kukhulupilila n’kofunika. Komabe, tifunikanso kudziŵa kuti kungokhulupilila kuti Yesu aliko sikokwanila. Malinga ndi buku lakuti Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words, mau amene Yohane anagwilitsila nchito amatanthauza “kudalila wina wake kapena cina cake, osati cabe kukhulupilila.” Kuti munthu akhale paubwenzi ndi Mulungu sayenela cabe kudziŵa kuti Yesu ndi Mpulumutsi. Ayenelanso kuyesetsa kucita zimene Yesu anaphunzitsa. Ngati sacitapo kanthu, cikhulupililo cake cimakhala copanda phindu. Baibulo limati: “Cikhulupililo copanda nchito zake ndi cakufa.” (Yakobo 2:26) M’mau ena, munthuyo ayenela kukhulupilila Yesu, kutanthauza kuti ayenela kutsatila zimene amakhulupilila paumoyo wake.

Pofotokoza mfundoyi Paulo anati: “Cikondi cimene Kristu ali naco cimatikakamiza, cifukwa tatsimikiza kuti munthu mmodzi [Yesu] anafela anthu onse, . . . Iye anafelanso onse kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha, koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafela n’kuukitsidwa.” (2 Akorinto 5:14, 15) Kuyamikila nsembe ya Yesu ndi mtima wonse kuyenela kutipangitsa kusintha umoyo wathu. Tisakhale ndi moyo wofuna kudzisangalatsa tokha koma tikhale ndi moyo wosangalatsa Yesu amene anatifela. Zimenezi zitanthauza kuti kutsatila ziphunzitso za Yesu kuyenela kukhala patsogolo paumoyo wathu. Kusintha kumeneku kudzakhudza makhalidwe athu, zosankha zathu, ndi zilizonse zimene timacita. Kodi anthu amene amakhulupilila Yesu adzapeza madalitso otani?

“ASAONONGEKE, KOMA AKHALE NDI MOYO WOSATHA”

Mbali yothela ya lemba la Yohane 3:16 limafotokoza zimene Mulungu walonjeza anthu amene amakhulupilila nsembe ya dipo ndi kutsatila miyezo ya Mulungu paumoyo wao. Mulungu afuna kuti anthu okhulupilika amenewa “asaonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” Koma anthu amene adzapindula ndi cikondi ca Mulungu ali ndi ziyembekezo zosiyana.

Yesu analonjeza gulu lina kuti lidzakhala ndi moyo kumwamba. Iye anauza ophunzila ake okhulupilika kuti adzapita kukawakonzela malo kuti akalamulile ndi iye mu ulemelelo wake. (Yohane 14:2, 3; Afilipi 3:20, 21) Anthu amene adzapita kumwamba “adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, ndipo adzalamulila monga mafumu limodzi naye zaka 1,000.”—Chivumbulutso 20:6.

Otsatila a Kristu ocepa cabe ndi amene adzakhala ndi mwai umenewu. Ndipo Yesu anati: “Musaope, kagulu ka nkhosa inu, cifukwa Atate wanu wavomeleza kukupatsani Ufumu.” (Luka 12:32) Kodi anthu a “kagulu ka nkhosa” ndi angati? Lemba la Chivumbulutso 14:1, 4 limati: “Ndinaona Mwanawankhosa ataimilila paphili la Ziyoni. Limodzi naye panali enanso 144,000 olembedwa dzina lake ndi dzina la Atate wake pamphumi pao. . . . Iwowa anagulidwa kucokela mwa anthu, monga zipatso zoyambilila zopelekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.” Poyelekezela ndi mabiliyoni ambili a anthu amene akhalapo ndi moyo, a 144,000 ndi “kagulu ka nkhosa” kocepa. Popeza io adzakhala mafumu, kodi adzalamulila ndani?

Yesu ananenanso za gulu laciŵili la anthu okhulupilika amene adzapindula ndi madalitso a Ufumu wa kumwamba. Malinga ndi Yohane 10:16, Yesu anati: “Ndili ndi nkhosa zina zimene sizili za khola ili, zimenezonso ndiyenela kuzibweletsa. Zidzamva mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi m’busa mmodzi.” “Nkhosa” zimenezo zikuyembekezela moyo wosatha padziko lapansi, umene Adamu ndi Hava akanakhala nao. Kodi timadziŵa bwanji kuti nkhosazi zidzakhala padziko lapansi?

Mavesi ambili m’Baibulo amaonetsa mmene moyo udzakhalila m’Paladaiso padziko lapansi. Kuti mutsimikize zimenezi, tsegulani Baibulo lanu ndi kuŵelenga Malemba awa: Salimo 37:9-11; 46:8, 9; 72:7, 8, 16; Yesaya 35:5, 6; 65:21-23; Mateyu 5:5; Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 21:4. Malembawa amanena kuti nkhondo, njala, matenda ndi imfa zidzatha. Amanenanso za nthawi pamene anthu abwino adzamanga nyumba zao-zao, adzalima minda ndi kulela ana m’mikhalidwe yabwino.a Kodi simumasangalala ndi malonjezo amenewa? Tili ndi zifukwa zomveka zokhulupilila kuti posacedwapa malonjezo amenewa adzakwanilitsidwa.

MULUNGU WAKUCITILANI ZAMBILI

Mukaganizila zimene Mulungu wakucitilani ndi zimene wacitila anthu onse, mungavomeleze kuti iye wacita zambili. Tili ndi moyo, nzelu, thanzi ndi zinthu zocilikiza moyo. Koposa izi, mphatso ya Mulungu ya nsembe ya Yesu, amene anatifela, ingacititse kuti tikalandile madalitso oculuka monga mmene taphunzilila pa Yohane 3:16.

Kukhala ndi moyo wosatha m’mikhalidwe ya mtendele ndi yabwino popanda kudwala, nkhondo, njala kapena imfa, kudzacititsa kuti tikasangalale ndi madalitso kwamuyaya. Kaya mudzalandila madalitso amenewa kapena ai, zidzadalila inu. Koma funso ndi lakuti, Kodi inuyo mukumucitila ciani Mulungu?

a Kuti mudziŵe zambili ponena za maulosi amenewa, onani nkhani 3 m’buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani