-
Mlaliki 2:4-8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Ndinagwira ntchito zikuluzikulu.+ Ndinamanga nyumba zambirimbiri.+ Ndinalima minda ya mpesa yambirimbiri.+ 5 Ndinakonza minda yokongola komanso malo odzalamo maluwa ndi mitengo. Ndipo ndinadzalamo mitengo ya zipatso zosiyanasiyana. 6 Ndinapanga madamu a madzi kuti ndizithirira mitengo imene inamera mʼnkhalango yanga. 7 Ndinali ndi antchito aamuna ndi aakazi+ komanso ndinali ndi antchito amene anabadwira mʼnyumba mwanga.* Ndinalinso ndi ziweto zochuluka zedi, ngʼombe ndi nkhosa.+ Zinali zambiri kuposa za onse amene anakhalapo mu Yerusalemu ine ndisanakhalepo. 8 Ndinapeza siliva ndi golide wambiri,+ chuma chimene mafumu amakhala nacho* ndiponso chimene chimapezeka mʼzigawo za dziko.+ Ndinali ndi oimba aamuna ndi aakazi. Ndinalinso ndi akazi ambiri, omwe amasangalatsa kwambiri mtima wa amuna.
-