Mlaliki
7 Mbiri yabwino imaposa mafuta onunkhira,+ ndipo tsiku lomwalira limaposa tsiku lobadwa.+ 2 Ndi bwino kupita kunyumba yamaliro kusiyana ndi kupita kunyumba yamadyerero,+ chifukwa amenewo ndiwo mapeto a anthu onse. Chotero munthu amene ali moyo aziganizira zimenezi mumtima mwake. 3 Kuli bwino kumva chisoni kusiyana ndi kuseka,+ pakuti nkhope yachisoni imachititsa kuti mtima wa munthu ukhale wabwino.+ 4 Mtima wa anthu anzeru umakhala m’nyumba yamaliro,+ koma mtima wa anthu opusa umakhala m’nyumba yachisangalalo.+
5 Kuli bwino kumvetsera munthu wanzeru akamakudzudzula,+ kusiyana ndi kumvetsera nyimbo ya anthu opusa.+ 6 Pakuti kuseka kwa anthu opusa+ kumamveka ngati kuthetheka kwa minga zomwe zikuyaka pansi pa mphika. Izinso n’zachabechabe. 7 Kuponderezedwa kumapangitsa munthu wanzeru kuchita zinthu zopanda nzeru,+ ndipo mphatso+ ikhoza kuwononga mtima wa munthu.+
8 Mapeto a chinthu amakhala bwino kuposa chiyambi chake,+ ndipo munthu woleza mtima ndi wabwino kuposa munthu wodzikuza.+ 9 Usamafulumire kukwiya mumtima mwako,+ pakuti anthu opusa ndi amene sachedwa kupsa mtima.+
10 Usanene kuti: “N’chifukwa chiyani kale zinthu zinali bwino kuposa masiku ano?”+ Pakuti si nzeru+ kufunsa funso lotere.
11 Munthu wanzeru akalandira cholowa zimakhala bwino, ndipo nzeru zimapindulitsa anthu amene ali padziko lapansi.+ 12 Pakuti nzeru zimateteza+ monga mmene ndalama zimatetezera,+ koma ubwino wa kudziwa zinthu ndi wakuti nzeru zimasunga moyo wa eni nzeruzo.+
13 Taona ntchito+ ya Mulungu woona, pakuti ndani angathe kuwongola zinthu zimene iye anazikhotetsa?+ 14 Pa tsiku labwino ukhale munthu wabwino,+ ndipo pa tsiku latsoka uzindikire kuti Mulungu woona anapanga masiku onsewa mofanana,+ ndi cholinga chakuti anthu asadziwe chilichonse chimene chidzachitike pambuyo pawo.+
15 Ndaona zinthu zonse m’masiku anga opanda pake.+ Pali munthu wolungama amene amawonongeka akuchita zolungama,+ ndipo pali munthu woipa amene amakhala ndi moyo wautali akuchitabe zoipa.+
16 Usakhale wolungama mopitirira muyezo+ kapena kudzionetsera kuti ndiwe wanzeru kwambiri,+ kuopera kuti ungadzibweretsere chiwonongeko.+ 17 Usakhale woipa mopitirira muyezo,+ komanso usakhale wopusa.+ Uferenji mwamsanga?+ 18 Ndi bwino kuti usunge malangizo oyambawo, ndipo usasiye malangizo achiwiriwo.+ Pakuti munthu amene amaopa Mulungu adzamvera malangizo onsewa.+
19 Nzeru zimapangitsa munthu kukhala wamphamvu kuposa atsogoleri 10 amphamvu amene ali mumzinda.+ 20 Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa.+
21 Komanso usamaganizire kwambiri mawu onse amene anthu amalankhula,+ kuti ungamve wantchito wako akukunenera zoipa.+ 22 Pakuti mtima wako ukudziwa bwino kuti ngakhale iweyo wanenerapo anthu ena zoipa kambirimbiri.+
23 Zonsezi ndinazifufuza mwanzeru ndipo ndinati: “Ndidzakhala wanzeru.” Koma nzeruzo zinatalikirana nane.+ 24 Zimene zinachitika kale n’zapatali ndiponso n’zozama kwambiri. Ndani angazimvetse?+ 25 Ineyo ndinaganiziranso mumtima mwanga+ kuti ndidziwe, ndifufuze, ndiponso ndifunefune nzeru.+ Ndinafunanso kudziwa zimene zimayambitsa zinthu,+ ndiponso kudziwa kuipa kwa kupusa ndi uchitsiru wa misala.+ 26 Ndipo izi n’zimene ndinapeza: Mkazi amene ali ngati ukonde wosakira nyama, amene mtima wake uli ngati khoka, amene manja ake ali ngati unyolo,+ ndi wowawa kuposa imfa.+ Munthu amakhala wabwino pamaso pa Mulungu woona akapulumuka kwa mkaziyo, koma amachimwa akagwidwa naye.+
27 Wosonkhanitsa+ anati: “Taona zimene ndapeza. Ndafufuza chinthu chimodzichimodzi kuti ndidziwe tanthauzo la zonsezi,+ 28 limene ndakhala ndikulifunafuna koma osalipeza. Pa anthu 1,000, ndapezapo mwamuna mmodzi yekha wowongoka mtima,+ koma pa anthu onsewa sindinapezepo mkazi wowongoka mtima.+ 29 Zimene ndapeza n’zakuti, Mulungu woona anapanga anthu owongoka mtima,+ koma anthuwo asankha njira zina zambirimbiri.”+