1 Timoteyo
Ngati munthu aliyense akuyesetsa kuti akhale woyang’anira,+ akufuna ntchito yabwino. 2 Choncho woyang’anira akhale wopanda chifukwa chomunenezera,+ mwamuna wa mkazi mmodzi, wosachita zinthu mopitirira malire,+ woganiza bwino,+ wadongosolo,+ wochereza alendo,+ ndiponso wotha kuphunzitsa.+ 3 Asakhale munthu womwa mowa mwauchidakwa,*+ kapena wandewu,+ koma wololera.+ Asakhale waukali,+ kapena wokonda ndalama.+ 4 Akhale mwamuna woyang’anira bwino banja lake+ ndiponso akhale woti ana ake amamumvera ndi mtima wonse.+ 5 (Ndithudi, ngati munthu sadziwa kuyang’anira banja lake, ndiye mpingo wa Mulungu angausamalire bwanji?) 6 Asakhale wotembenuka kumene,+ kuopera kuti angakhale wotukumuka chifukwa cha kunyada,+ n’kulandira chiweruzo chofanana ndi chimene Mdyerekezi analandira.+ 7 Komanso, akhale woti ngakhale anthu akunja* akumuchitira umboni wabwino,+ kuti asatonzedwe ndi kukodwa mumsampha+ wa Mdyerekezi.
8 Nawonso atumiki othandiza+ akhale opanda chibwana, osanena pawiri, osakonda kumwa vinyo wambiri, ndiponso osakonda kupeza phindu mwachinyengo.+ 9 Akhale ogwira chikhulupiriro mwamphamvu, chimene ndi chinsinsi chopatulika+ cha Mulungu, ali ndi chikumbumtima choyera.+
10 Ndiponso, amenewa ayesedwe+ kaye ngati ali oyenerera, ndiyeno atumikire monga atumiki, popeza ndi opanda chifukwa chowanenezera.+
11 Nawonso amayi akhale opanda chibwana, osati amiseche.+ Akhale ochita zinthu mosapitirira malire,+ ndi okhulupirika m’zinthu zonse.+
12 Atumiki othandiza akhale amuna a mkazi mmodzi,+ oyang’anira bwino ana awo ndi mabanja awo.+ 13 Pakuti amuna otumikira bwino amakhala ndi mbiri yabwino+ ndi ufulu waukulu wa kulankhula+ za chikhulupiriro, mwa Khristu Yesu.
14 Ndikukulembera zimenezi, ngakhale kuti ndikuyembekezera kuti ndibwera kwa iwe posachedwapa.+ 15 Koma ngati ndingachedwe, ndalemba izi kuti udziwe mmene uyenera kuchitira m’nyumba ya Mulungu,+ imene ndi mpingo wa Mulungu wamoyo. Mpingowo ndi umene umalimbikitsa ndi kuteteza+ choonadi. 16 Ndithudi, chinsinsi chopatulikachi+ chokhudza kukhala odzipereka kwa Mulungu n’chachikulu ndithu: ‘Iye anaonekera ngati munthu,+ anaonedwa kuti ndi wolungama pamene anali mzimu,+ anaonekera kwa angelo,+ analalikidwa kwa mitundu ya anthu,+ anthu padziko lapansi anamukhulupirira,+ ndiponso analandiridwa kumwamba mu ulemerero.’+