Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 20:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 “‘Munthu wotembenukira kwa olankhula ndi mizimu+ ndi olosera zam’tsogolo,+ komwe n’kuchita mosakhulupirika kwa ine,* ndidzam’kana ndithu ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+

  • Deuteronomo 18:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 kapena wolodza* ena,+ aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu,+ wolosera zam’tsogolo+ kapena aliyense wofunsira kwa akufa.+

  • 1 Samueli 28:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Pamapeto pake, Sauli anauza atumiki ake kuti: “Ndifufuzireni mkazi waluso polankhula ndi mizimu,+ ndipo ine ndipita kukalankhula naye.” Pamenepo atumiki ake anamuuza kuti: “Ku Eni-dori alipo mkazi waluso polankhula ndi mizimu.”+

  • 1 Mbiri 10:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Choncho Sauli anafa chifukwa cha kusakhulupirika kwake popeza anachita zosakhulupirika+ kwa Yehova. Iye sanasunge mawu a Yehova komanso anapita kukafunsa kwa wolankhula ndi mizimu.+

  • 2 Mbiri 33:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Manase anatentha* ana ake aamuna pamoto+ m’chigwa cha mwana wa Hinomu,+ ndipo ankachita zamatsenga,+ ankawombeza,+ ankachita zanyanga,+ ndiponso anaika anthu olankhula ndi mizimu+ ndi olosera zam’tsogolo.+ Iye anachita zinthu zambiri zoipa pamaso pa Yehova ndiponso zomukwiyitsa.+

  • Yesaya 8:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Akakuuzani anthu inu kuti: “Funsirani kwa anthu olankhula ndi mizimu+ kapena kwa anthu amene ali ndi mzimu wolosera zam’tsogolo, omwe amalira ngati mbalame+ ndiponso amalankhula motsitsa mawu,” kodi mtundu uliwonse wa anthu suyenera kufunsira kwa Mulungu wake?+ Kodi tizifunsira kwa anthu akufa kuti athandize anthu amoyo?+

  • Agalatiya 5:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 kupembedza mafano, kuchita zamizimu,+ udani, ndewu, nsanje, kupsa mtima, mikangano, kugawikana, magulu ampatuko,

  • Chivumbulutso 21:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Koma amantha, opanda chikhulupiriro,+ odetsedwa amenenso amachita zinthu zonyansa,+ opha anthu,+ adama,+ ochita zamizimu, opembedza mafano,+ ndi onse abodza,+ gawo lawo lidzakhala m’nyanja yoyaka moto+ ndi sulufule.+ Nyanja imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena