5 Ndiyeno amuna a ku Giliyadi anakatchinga powolokera Yorodano+ anthu a ku Efuraimu asanafike. Anthu othawa a ku Efuraimu akanena kuti: “Ndiloleni ndiwoloke,” pamenepo amuna a ku Giliyadi anali kumufunsa kuti: “Kodi ndiwe wa ku Efuraimu?” Akayankha kuti: “Ayi!”