Salimo 18:43 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 43 Inu mudzandipulumutsa kwa anthu a mtundu wanga onditola zifukwa.+Mudzandiika kukhala mtsogoleri wa mitundu yonse.+Anthu amene sindikuwadziwa adzanditumikira.+ Yesaya 55:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Iwe udzaitana mtundu umene sukuudziwa,+ ndipo anthu a mtundu wosakudziwa adzathamangira kwa iwe+ chifukwa cha Yehova Mulungu wako,+ ndiponso chifukwa cha Woyera wa Isiraeli,+ pakuti iye adzakukongoletsa.+ Yesaya 65:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 65 “Ine ndalola kuti anthu amene sanafunse za ine+ andifunefune.+ Ndalola kuti anthu amene sanandifunefune andipeze.+ Ndanena kuti, ‘Ndili pano, ndili pano!’+ kwa mtundu umene sunaitane pa dzina langa.+ Hoseya 2:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Pamenepo ndidzamufesa ngati mbewu zanga padziko lapansi.+ Ndidzachitira chifundo amene sanasonyezedwe chifundo+ ndipo ndidzauza anthu amene si anthu anga kuti: “Inu ndinu anthu anga,”+ ndipo iwo adzayankha kuti: “Inu ndinu Mulungu wathu.”’”+ Machitidwe 15:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Sumeoni+ wafotokoza bwino mmene Mulungu anacheukira anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti mwa iwo atengemo anthu odziwika ndi dzina lake.+
43 Inu mudzandipulumutsa kwa anthu a mtundu wanga onditola zifukwa.+Mudzandiika kukhala mtsogoleri wa mitundu yonse.+Anthu amene sindikuwadziwa adzanditumikira.+
5 Iwe udzaitana mtundu umene sukuudziwa,+ ndipo anthu a mtundu wosakudziwa adzathamangira kwa iwe+ chifukwa cha Yehova Mulungu wako,+ ndiponso chifukwa cha Woyera wa Isiraeli,+ pakuti iye adzakukongoletsa.+
65 “Ine ndalola kuti anthu amene sanafunse za ine+ andifunefune.+ Ndalola kuti anthu amene sanandifunefune andipeze.+ Ndanena kuti, ‘Ndili pano, ndili pano!’+ kwa mtundu umene sunaitane pa dzina langa.+
23 Pamenepo ndidzamufesa ngati mbewu zanga padziko lapansi.+ Ndidzachitira chifundo amene sanasonyezedwe chifundo+ ndipo ndidzauza anthu amene si anthu anga kuti: “Inu ndinu anthu anga,”+ ndipo iwo adzayankha kuti: “Inu ndinu Mulungu wathu.”’”+
14 Sumeoni+ wafotokoza bwino mmene Mulungu anacheukira anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti mwa iwo atengemo anthu odziwika ndi dzina lake.+