Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 18:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Iye anadalira Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ Panalibenso mfumu ina yofanana naye pamafumu onse a Yuda+ amene anakhalapo iye asanakhale mfumu, ngakhalenso amene anakhalapo iye atafa.+

  • 1 Mbiri 5:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Pa nkhondoyo iwo anathandizidwa moti Ahagara ndi onse amene anali nawo anaperekedwa m’manja mwawo, popeza anapempha Mulungu kuti awathandize+ ndipo iye anamva kupembedzera kwawo chifukwa anam’khulupirira.+

  • 2 Mbiri 16:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Kodi Aitiyopiya+ ndi Alibiya+ sanali gulu lankhondo lalikulu, la anthu ambiri, magaleta ambiri, ndi okwera pamahatchi ambirinso?+ Chifukwa chakuti munadalira Yehova, kodi iye sanawapereke m’manja mwanu?+

  • Salimo 22:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Iwo anali kufuulira inu,+ ndipo anali kupulumuka.+

      Anali kudalira inu, ndipo simunawachititse manyazi.+

  • Salimo 37:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako,+

      Umudalire+ ndipo iye adzachitapo kanthu.+

  • Salimo 146:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Wodala ndi munthu amene thandizo lake limachokera kwa Mulungu wa Yakobo,+

      Amene chiyembekezo chake chili mwa Yehova Mulungu wake,+

  • Nahumu 1:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Yehova ndi wabwino+ ndipo ndi malo achitetezo+ pa tsiku la nsautso.+

      Amadziwa amene amathawira kwa iye kuti apeze chitetezo.+

  • 1 Timoteyo 4:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pa chifukwa chimenechi, tikugwira ntchito mwakhama ndiponso mwamphamvu,+ chifukwa chiyembekezo+ chathu chili mwa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi+ wa anthu a mtundu uliwonse,+ koma makamaka okhulupirika.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena