Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Esitere 9:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 pa tsiku la 13 la mwezi wa Adara. Ndiyeno pa tsiku la 14 la mweziwo anapuma ndi kulisandutsa tsiku laphwando+ ndi lachikondwerero.+

  • Salimo 18:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Pakuti inu Yehova mudzandiyatsira nyale yanga,+

      Mulungu wanga adzandiunikira mu mdima.+

  • Salimo 30:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Chifukwa mkwiyo wa Mulungu sukhalitsa pa munthu,+

      Koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse.+

      Usiku kumakhala kulira,+ koma m’mawa kumakhala kufuula ndi chisangalalo.+

  • Salimo 97:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Kuwala kwaunikira wolungama,+

      Ndipo anthu owongoka mtima akusangalala.+

  • Miyambo 11:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Mudzi umakondwera chifukwa cha makhalidwe abwino a anthu olungama,+ koma anthu oipa akawonongeka pamakhala mfuu yachisangalalo.+

  • Yesaya 30:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Kuwala kwa mwezi wathunthu kudzakhala ngati kuwala kwa dzuwa lowala kwambiri. Kuwala kwa dzuwa lowala kwambiri kudzawonjezereka maulendo 7+ ndipo kudzakhala ngati kuwala kwa masiku 7. Zimenezi zidzachitika m’tsiku limene Yehova adzachiritse mtundu wake wovulala+ ndi kupoletsa+ chilonda choopsa cha anthu ake, amene iyeyo anawavulaza powalanga.

  • Mika 7:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Iwe mdani wanga,+ usasangalale chifukwa cha zimene zandichitikira. Ngakhale kuti ndagwa, ndidzadzuka ndithu.+ Ngakhale kuti ndili mumdima,+ Yehova adzakhala kuwala kwanga.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena