Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 30:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 “Koma iweyo utenge mafuta awa onunkhira, abwino koposa:+ madontho oundana a mule*+ masekeli 500, sinamoni*+ wonunkhira bwino hafu ya muyezo wa mule, kapena kuti masekeli 250, ndi kalamasi* wonunkhira+ wokwana masekeli 250.

  • Esitere 2:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Mtsikana aliyense anali kukaonekera kwa Mfumu Ahasiwero pambuyo poti am’chitira zonse zimene amayenera kum’chitira pa miyezi 12 malinga ndi lamulo lokhudza akazi. Atsikanawo anali kuwapaka mafuta a mule*+ miyezi 6 kenako anali kuwapaka mafuta a basamu+ pamodzi ndi mafuta enanso okongoletsa miyezi inanso 6. Akachita zimenezi ndiye kuti amaliza dongosolo lonse lowakongoletsera.

  • Salimo 45:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Zovala zako zonse ndi zonunkhira mafuta a mule, aloye ndi kasiya.*+

      Umasangalala ndi nyimbo zoimbidwa ndi zipangizo za zingwe, kuchokera m’chinyumba chachikulu cha mfumu, chokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu.+

  • Nyimbo ya Solomo 4:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 “Nthawi ya kamphepo kayaziyazi isanakwane+ ndiponso mithunzi isanachoke, ndipita kuphiri la mule ndiponso kuphiri la lubani.”+

  • Nyimbo ya Solomo 5:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Masaya ake ali ngati bedi la m’munda la maluwa onunkhira,+ ndiponso ngati nsanja zomangidwa ndi zitsamba zonunkhira. Milomo yake ili ngati maluwa amene akuchucha mafuta a mule.+

  • Yohane 19:39
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 39 Nayenso Nikodemo, munthu amene anabwera kwa iye usiku poyamba paja, anabwera atatenga mule wosakaniza ndi aloye, wopitirira makilogalamu 32.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena