Ekisodo 15:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Ndi mulungu wina uti amene angafanane nanu, inu Yehova?+Ndinu woyera kopambana, ndani angafanane ndi inu?+Ndinu woyenera kuopedwa+ ndi kukuimbirani nyimbo zotamanda.+ Inu ndinu wochita zodabwitsa.+ Ezara 9:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli ndinu wolungama+ chifukwa ife tatsala monga anthu opulumuka lero. Taima pamaso panu m’machimo athu,+ ngakhale kuti n’zosatheka kuima pamaso panu chifukwa cha machimo athuwo.”+ Salimo 145:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Iwo adzalankhula mosefukira za kuchuluka kwa ubwino wanu,+Ndipo adzafuula mokondwera chifukwa cha chilungamo chanu.+ Chivumbulutso 15:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Iwo akuimba nyimbo ya Mose+ kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa,+ yakuti: “Ntchito zanu n’zazikulu ndi zodabwitsa,+ inu Yehova Mulungu Wamphamvuyonse.+ Njira zanu ndi zolungama ndi zoona,+ inu Mfumu yamuyaya.+ Chivumbulutso 19:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 chifukwa ziweruzo zake ndi zoona ndi zolungama.+ Pakuti iye waweruza hule lalikulu limene linaipitsa dziko lapansi ndi dama* lake, ndipo walibwezera chifukwa cha magazi a akapolo ake, amene hulelo linapha.”+
11 Ndi mulungu wina uti amene angafanane nanu, inu Yehova?+Ndinu woyera kopambana, ndani angafanane ndi inu?+Ndinu woyenera kuopedwa+ ndi kukuimbirani nyimbo zotamanda.+ Inu ndinu wochita zodabwitsa.+
15 Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli ndinu wolungama+ chifukwa ife tatsala monga anthu opulumuka lero. Taima pamaso panu m’machimo athu,+ ngakhale kuti n’zosatheka kuima pamaso panu chifukwa cha machimo athuwo.”+
7 Iwo adzalankhula mosefukira za kuchuluka kwa ubwino wanu,+Ndipo adzafuula mokondwera chifukwa cha chilungamo chanu.+
3 Iwo akuimba nyimbo ya Mose+ kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa,+ yakuti: “Ntchito zanu n’zazikulu ndi zodabwitsa,+ inu Yehova Mulungu Wamphamvuyonse.+ Njira zanu ndi zolungama ndi zoona,+ inu Mfumu yamuyaya.+
2 chifukwa ziweruzo zake ndi zoona ndi zolungama.+ Pakuti iye waweruza hule lalikulu limene linaipitsa dziko lapansi ndi dama* lake, ndipo walibwezera chifukwa cha magazi a akapolo ake, amene hulelo linapha.”+