Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 21:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Zitatero, Abulahamu anabzala mtengo wa bwemba pa Beere-seba, n’kuitanirapo dzina la Yehova,+ Mulungu wanthawi zonse.+

  • Deuteronomo 33:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Mulungu wakale lomwe ndiwo malo ako obisalamo,+

      Ndipo iwe uli m’manja amene adzakhalapo mpaka kalekale.+

      Adzapitikitsa mdani pamaso pako,+

      Ndipo adzanena kuti, ‘Awononge!’+

  • Salimo 90:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Mapiri asanabadwe,+

      Kapena musanakhazikitse dziko lapansi+ ndi malo okhalapo anthu,*+

      Inu ndinu Mulungu kuyambira kalekale mpaka kalekale.+

  • Yesaya 57:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Pakuti Wapamwamba ndi Wokwezeka,+ yemwe adzakhalepo kwamuyaya+ ndiponso yemwe dzina lake ndi loyera,+ wanena kuti: “Ine ndimakhala kumwamba pamalo oyera.+ Ndimakhalanso ndi munthu wopsinjika ndi wa mtima wodzichepetsa,+ kuti nditsitsimutse mtima wa anthu onyozeka ndiponso kuti nditsitsimutse mtima wa anthu opsinjika.+

  • Yeremiya 10:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Koma Yehova ndi Mulungu woonadi.+ Iye ndi Mulungu wamoyo+ ndipo ndi Mfumu mpaka kalekale.+ Dziko lapansi lidzagwedezeka ndi mkwiyo wake,+ ndipo palibe mitundu ya anthu imene idzalimbe pamene iye akuidzudzula.+

  • Aroma 16:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Koma tsopano chinsinsi chopatulika chimenechi chaonetsedwa+ ndipo chadziwika pakati pa mitundu yonse ya anthu kudzera m’malemba aulosi. Zimenezi n’zogwirizana ndi lamulo la Mulungu wokhalako kwamuyaya. Cholinga chake n’chakuti anthu a mitundu yonse amukhulupirire ndi kumumvera mwa chikhulupiriro.+

  • 1 Timoteyo 1:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Kwa Mfumu yamuyaya,+ imene siifa,+ yosaoneka,+ yekhayo amene ali Mulungu,+ kwa iyeyo kupite ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya.+ Ame.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena