Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 2:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Onse olimbana ndi Yehova adzagwidwa ndi mantha.+

      Motsutsana nawo, iye adzagunda ngati mabingu kumwamba.+

      Yehova mwiniwake adzaweruza dziko lonse lapansi,+

      Kuti apereke mphamvu kwa mfumu yake,+

      Ndi kuti akweze nyanga ya wodzozedwa wake.”+

  • Salimo 67:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Mitundu ya anthu isangalale ndi kufuula mokondwera,+

      Pakuti inu mudzaweruza anthu molungama.+

      Ndipo mudzatsogolera mitundu ya anthu padziko lapansi. [Seʹlah.]

  • Salimo 96:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Pakuti iye wabwera.+

      Iye wabwera kudzaweruza dziko lapansi.+

      Adzaweruza dziko mwachilungamo,+

      Ndipo adzaweruza mitundu ya anthu mokhulupirika.+

  • Yesaya 2:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Mulungu adzakhala woweruza pakati pa mitundu+ ndipo adzakonza zinthu+ zokhudza mitundu yambiri ya anthu.+ Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo.+ Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.+

  • Machitidwe 17:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Chifukwa wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweruza+ m’chilungamo dziko lapansi kumene kuli anthu, kudzera mwa munthu amene iye wamuika. Ndipo wapereka chitsimikizo kwa anthu onse mwa kumuukitsa+ kwa akufa.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena