6 Yehova Mulungu wanu adzachita mdulidwe wa mitima yanu+ ndi mitima ya ana anu,+ kuti muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.+
7 Ndidzawapatsa mtima wodziwa kuti ine ndine Yehova.+ Iwo adzakhala anthu anga+ ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo pakuti adzabwerera kwa ine ndi mtima wawo wonse.+
29 Koma Myuda ndi amene ali wotero mkati,+ ndipo mdulidwe wake ndi wa mumtima+ wochitidwa ndi mzimu, osati ndi malamulo olembedwa.+ Munthu woteroyo satamandidwa+ ndi anthu koma ndi Mulungu.+
22 Chotero, thawa zilakolako zaunyamata,+ koma tsatira chilungamo,+ chikhulupiriro, chikondi, ndi mtendere+ limodzi ndi anthu oitana pa Ambuye ndi mtima woyera.+