Levitiko 26:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Mizinda yanu ndidzaiwononga ndi lupanga+ ndipo malo anu opatulika adzakhala opanda anthu,+ komanso sindidzalandira nsembe zanu zafungo lokhazika mtima pansi.+ 1 Mafumu 9:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 ineyo ndidzachotsa Aisiraeli padziko limene ndawapatsa+ ndipo nyumba imene ndaiyeretsa ndi dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga.+ Aisiraeli adzawapekera mwambi+ ndi kuwatonza pakati pa mitundu yonse ya anthu. Salimo 69:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Msasa wawo wokhala ndi mpanda ukhale bwinja,+Ndipo m’mahema awo musapezeke munthu wokhalamo.+ Yesaya 1:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Dziko lanu lawonongedwa.+ Mizinda yanu yatenthedwa ndi moto,+ ndipo alendo akudya zokolola zochokera munthaka yanu, inu mukuona.+ Chilichonse chawonongeka ngati mmene zimakhalira adani akalanda dziko.+ Yeremiya 12:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 “Ndasiya nyumba yanga.+ Ndasiya cholowa changa.+ Wokondedwa wanga ndamupereka m’manja mwa adani ake.+ Yeremiya 22:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 “‘Koma mukapanda kumvera mawu amenewa, ndikulumbira pali ine mwini+ kuti nyumba iyi idzakhala bwinja,’ watero Yehova.+ Mika 3:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Chotero Ziyoni adzagawulidwa ngati munda chifukwa cha anthu inu ndipo Yerusalemu adzangokhala milu ya mabwinja.+ Phiri la nyumba ya Mulungu lidzakhala ngati zitunda za m’nkhalango.
31 Mizinda yanu ndidzaiwononga ndi lupanga+ ndipo malo anu opatulika adzakhala opanda anthu,+ komanso sindidzalandira nsembe zanu zafungo lokhazika mtima pansi.+
7 ineyo ndidzachotsa Aisiraeli padziko limene ndawapatsa+ ndipo nyumba imene ndaiyeretsa ndi dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga.+ Aisiraeli adzawapekera mwambi+ ndi kuwatonza pakati pa mitundu yonse ya anthu.
7 Dziko lanu lawonongedwa.+ Mizinda yanu yatenthedwa ndi moto,+ ndipo alendo akudya zokolola zochokera munthaka yanu, inu mukuona.+ Chilichonse chawonongeka ngati mmene zimakhalira adani akalanda dziko.+
7 “Ndasiya nyumba yanga.+ Ndasiya cholowa changa.+ Wokondedwa wanga ndamupereka m’manja mwa adani ake.+
5 “‘Koma mukapanda kumvera mawu amenewa, ndikulumbira pali ine mwini+ kuti nyumba iyi idzakhala bwinja,’ watero Yehova.+
12 Chotero Ziyoni adzagawulidwa ngati munda chifukwa cha anthu inu ndipo Yerusalemu adzangokhala milu ya mabwinja.+ Phiri la nyumba ya Mulungu lidzakhala ngati zitunda za m’nkhalango.