34 Pa chifukwa chimenechi, tsopano ndikukutumizirani+ aneneri, anthu anzeru ndi aphunzitsi.+ Ena a iwo mudzawapha+ ndi kuwapachika, ndipo ena mudzawakwapula+ m’masunagoge mwanu ndi kuwazunza mumzinda ndi mzinda,
11 Ukudziwanso mazunzo ndi masautso amene ndinakumana nawo ku Antiokeya,+ ku Ikoniyo,+ ndi ku Lusitara.+ Komabe, Ambuye anandipulumutsa m’mazunzo onsewa.+