Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Miyambo 11:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Zipatso za munthu wolungama ndizo mtengo wa moyo,+ ndipo munthu wopulumutsa miyoyo ndi wanzeru.+

  • 2 Akorinto 1:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Tsopano ngati tili m’masautso, cholinga chake ndi choti inuyo mutonthozedwe ndi kupulumutsidwa.+ Ngati tikutonthozedwa, cholinga chake ndi choti inuyo mutonthozedwe kuti mupirire masautso amene ifenso tikukumana nawo.+

  • Afilipi 2:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ngakhale kuti ndikudzipereka ngati nsembe yachakumwa imene ikuthiridwa+ pansembe+ ndi pa ntchito yotumikira anthu imene chikhulupiriro chakupatsani,+ ndine wokondwa ndipo ndikukondwera+ ndi inu nonse.

  • Akolose 1:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Ndikusangalala tsopano ndi masautso amene ndikukumana nawo chifukwa cha inu.+ Ndipo inenso kumbali yanga, ndikuona kuti sindinazunzikebe mokwanira+ monga chiwalo cha thupi la Khristu, limene ndi mpingo.+

  • 1 Atesalonika 2:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Choncho popeza timakukondani kwambiri,+ tinali okonzeka kukupatsani uthenga wabwino wa Mulungu. Ndipotu osati uthenga wokha ayi, komanso miyoyo+ yathu yeniyeniyo, chifukwa tinakukondani kwambiri.+

  • Aheberi 13:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Muzimvera amene akutsogolera pakati panu+ ndipo muziwagonjera.+ Iwo amayang’anira miyoyo yanu monga anthu amene adzayankhe mlandu.+ Muziwamvera ndi kuwagonjera kuti agwire ntchito yawo mwachimwemwe, osati modandaula, pakuti akatero zingakhale zokuvulazani.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena