-
Chivumbulutso 8:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Mngelo woyamba analiza lipenga lake. Atatero, panaoneka matalala ndi moto,+ zosakanikirana ndi magazi. Zimenezi zinaponyedwa kudziko lapansi. Ndipo gawo limodzi mwa magawo atatu a dziko lapansi linapsa.+ Kuwonjezera pamenepo, gawo limodzi mwa magawo atatu a mitengo linapsa, komanso zomera zonse zobiriwira+ zinapsa.
-
-
Chivumbulutso 8:12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Ndiyeno mngelo wachinayi analiza lipenga lake. Atatero, gawo limodzi mwa magawo atatu a dzuwa linakanthidwa. Chimodzimodzinso gawo limodzi mwa magawo atatu a mwezi, ndi a nyenyezi. Zinatero kuti gawo limodzi mwa magawo atatu a zimenezi lichite mdima, ndi kuti gawo limodzi mwa magawo atatu a usana+ lisalandire kuunika,+ chimodzimodzinso usiku.
-