Deuteronomo
19 “Yehova Mulungu wako akadzawononga mitundu+ ya m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa, iwe n’kuwalandadi dzikolo ndi kukhala m’mizinda yawo ndi m’nyumba zawo,+ 2 udzadzipatulire mizinda itatu pakati pa dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa kuti likhale lako.+ 3 Udzadzilambulire njira yopita kumizindayo ndipo udzagawe dziko limene Yehova Mulungu wako wakupatsa kuti likhale lako. Dzikolo udzaligawe m’zigawo zitatu. Wopha munthu azithawira kumizinda imeneyo.+
4 “Nkhani ya munthu wopha mnzake amene angathawire kumeneko kuti akhale ndi moyo, izikhala yotere: Akapha munthu mosadziwa ndipo sanali kudana naye,+ 5 kapena akapita ndi mnzake kuthengo kukafuna nkhuni, ndipo wakweza dzanja lake kuti adule mtengo ndi nkhwangwa koma nkhwangwayo yaguluka mumpini wake+ n’kukantha mnzake ndi kumupha, wopha mnzakeyo azithawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi kuti akhale ndi moyo.+ 6 Akapanda kutero, wobwezera magazi+ angathamangitse wopha munthuyo ndi kum’peza, chifukwa mtunda ndi wautali. Pamenepo angamukanthe ndi kumupha chifukwa chakuti mtima wake ndi wodzaza ndi ukali, ngakhale kuti wopha mnzake mwangoziyo sanayenere kufa+ chifukwa sanali kudana naye. 7 N’chifukwa chake ndikukulamula kuti, ‘Udzipatulire mizinda itatu.’+
8 “Yehova Mulungu wanu akadzafutukula dera lanu malinga ndi zimene analumbirira makolo anu,+ n’kukupatsani dziko lonse limene analonjeza makolo anu kuti adzawapatsa,+ 9 chifukwa chakuti mwasunga malamulo onsewa amene ndikukupatsani lero mwa kuwatsatira, kuti muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi kuyenda m’njira zake nthawi zonse,+ pamenepo mudzawonjezere mizinda inanso itatu pa mizinda imeneyi,+ 10 kuti musakhetse magazi a munthu wosalakwa+ pakati pa dziko lanu limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani monga cholowa, kotero kuti musakhale ndi mlandu wa magazi.+
11 “Koma pakakhala munthu wodana+ ndi mnzake amene wabisalira ndi kuukira mnzakeyo panjira n’kumukantha ndipo wafa,+ iye n’kuthawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, 12 akulu a mumzinda wakwawo azitumiza anthu kukam’tenga kumeneko, ndipo azim’pereka m’manja mwa wobwezera magazi kuti afe ndithu.+ 13 Diso lako lisamumvere chisoni+ ndipo uzichotsa mlandu wa magazi a munthu wosalakwa mu Isiraeli+ kuti zinthu zikuyendere bwino.
14 “Usasunthe zizindikiro za malire a mnzako,+ makolo anu ataika kale malire a cholowa chimene udzalandira, m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa kuti ulitenge kukhala lako.
15 “Munthu akachita tchimo, mboni imodzi si yokwanira kutsimikizira kuti wachitadi cholakwacho kapena tchimo lililonse.+ Muzitsimikizira nkhaniyo mutamva umboni wapakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.+ 16 Munthu akakonzera mnzake chiwembu mwa kupereka umboni wonama wakuti waphwanya lamulo,+ 17 anthu awiri otsutsanawo aziima pamaso pa Yehova, pamaso pa ansembe ndi oweruza amene aziweruza masiku amenewo.+ 18 Pamenepo oweruza azifufuza nkhaniyo mosamala.+ Mboniyo ikapezeka kuti ndi yonama ndipo yaneneza m’bale wake mlandu wonama, 19 muziichitira zimene inafuna kuti zichitikire m’bale wakezo,+ ndipo muzichotsa woipayo pakati panu.+ 20 Chotero ena onse adzamva ndi kuchita mantha, ndipo sadzachitanso choipa chilichonse ngati chimenechi pakati panu.+ 21 Diso lako lisamumvere chisoni.+ Pazikhala moyo kulipira moyo, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, dzanja kulipira dzanja, phazi kulipira phazi.+