Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
31 Ndathawira kwa inu Yehova.+
Musalole kuti ndichite manyazi.+
Ndipulumutseni chifukwa cha chilungamo chanu.+
2 Tcherani khutu lanu kwa ine.+
Ndilanditseni mofulumira.+
Mukhale thanthwe lolimba kwa ine,+
Mukhale nyumba ya mpanda wolimba kuti mundipulumutse.+
3 Pakuti inu ndinu thanthwe langa ndi malo anga achitetezo.+
Chifukwa cha dzina lanu+ mudzanditsogolera ndi kundilozera njira.+
7 Ndidzakondwera ndi kusangalala chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha,+
Pakuti mwaona kusautsika kwanga.+
Mwadziwa zowawa zimene zandigwera,+
8 Simunandipereke m’manja mwa adani.+
Mwapondetsa phazi langa pamalo otakasuka.+
9 Ndikomereni mtima inu Yehova, pakuti ndasautsika kwambiri.+
Diso langa lafooka chifukwa cha chisoni,+ chimodzimodzinso moyo wanga ndi m’mimba mwanga.+
10 Chifukwa cha chisoni, moyo wanga watha,+
Ndipo chifukwa cha kuusa moyo kwanga, zaka zanga zafika kumapeto.+
Chifukwa cha zolakwa zanga, mphamvu zanga zafooka,+
Ndipo mafupa anga afooka.+
11 Ndakhala chitonzo+ pamaso pa onse odana nane,+
Ndipo kwa anthu oyandikana nawo ndakhala chitonzo chachikulu,+
Kwa anthu ondidziwa ndakhala woopsa.+
Akandiona ndili panja amandithawa.+
12 Ndaiwalidwa ngati munthu wakufa amene anthu sakumukumbukiranso.+
Ndakhala ngati chiwiya chosweka.+
13 Ndamva zinthu zoipa zimene anthu ambiri akunena,+
Ndamva zochititsa mantha kuchokera kumbali zonse.+
Akasonkhana pamodzi kundichitira upo,+
Amakonza chiwembu kuti achotse moyo wanga.+
14 Koma ine chikhulupiriro changa chili mwa inu Yehova.+
Ndipo ndikunena kuti: “Inu ndinu Mulungu wanga.”+
17 Inu Yehova, musalole kuti ndichite manyazi, pakuti ndaitana pa dzina lanu.+
Anthu oipa achite manyazi.+
Akhale chete m’Manda.+
18 Milomo yachinyengo isowe chonena,+
Milomo imene ikulankhula motsutsana ndi wolungama,+ yosadziletsa pa kudzikweza ndi kunyoza ena.+
19 Ubwino wanu,+ umene mwasungira anthu okuopani ndi wochuluka kwambiri!+
Ubwino umenewu mwapereka kwa anthu othawira kwa inu.
Mwaupereka kwa iwo, ana a anthu akuona.+
20 Mudzawabisa m’malo otetezeka pafupi ndi inu,+
Kuwachotsa pamaso pa anthu amene asonkhana pamodzi kuti awachitire chiwembu.+
Mudzawabisa mumsasa wanu kwa anthu ofuna kukangana nawo.+
22 Koma ine nditapanikizika ndinati:+
“Ndidzafafanizidwa kuchoka pamaso panu.”+
Ndithudi mwamva kuchonderera kwanga pamene ndinali kufuulira kwa inu kupempha thandizo.+