Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo pa Maluwa.*+ Salimo la Davide.
69 Ndipulumutseni, inu Mulungu, pakuti madzi afika m’khosi.+
2 Ndamila m’matope akuya, mmene mulibe malo oponda.+
Ndalowa m’madzi akuya,
Ndipo mtsinje wa madzi othamanga wandikokolola.+
3 Ndatopa ndi kufuula kwanga,+
Mawu asasa pammero panga.
Maso anga achita mdima poyembekezera Mulungu wanga.+
4 Anthu amene amadana nane popanda chifukwa achuluka kuposa tsitsi la m’mutu mwanga.+
Amene akufuna kunditsitsira kuli chete, chifukwa chodana nane popanda chifukwa, achuluka kwambiri.+
Ngakhale kuti sindine wakuba, anandikakamiza kubweza zinthu zimene zinabedwa.
6 Onse amene akuyembekezera inu asachite manyazi chifukwa cha ine,+
Inu Ambuye Wamkulu Koposa, Yehova wa makamu.+
Onse amene akufunafuna inu, asanyazitsidwe chifukwa cha ine,+
Inu Mulungu wa Isiraeli.+
9 Pakuti kudzipereka kwambiri panyumba yanu kwandidya,+
Ndipo mnyozo wa anthu amene akukutonzani wagwa pa ine.+
10 Ndipo ndinalira ndi kusala kudya chifukwa cha moyo wanga,+
Koma anthu anali kungonditonza chifukwa cha zimenezo.+
12 Anthu okhala kuchipata anayamba kundidera nkhawa,+
Ndipo anthu amene anali kumwa zakumwa zoledzeretsa anali kundinena mu nyimbo zawo.+
13 Koma ine ndinali kupemphera kwa inu Yehova,+
Pa nthawi yovomerezedwa, inu Mulungu.+
Ndiyankheni mwa kuchuluka kwa kukoma mtima kwanu kosatha, ndipo sonyezani kuti ndinudi mpulumutsi.+
14 Ndipulumutseni m’matope kuti ndisamire.+
Ndipulumutseni kwa anthu odana nane+ ndiponso ku madzi akuya.+
16 Ndiyankheni inu Yehova, pakuti kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwabwino.+
Ndicheukireni chifukwa chifundo chanu ndi chochuluka,+
17 Ndipo ine mtumiki wanu musandibisire nkhope yanu.+
Ndiyankheni mwamsanga, chifukwa ndasautsika kwambiri.+
19 Inu mwadziwa chitonzo changa, manyazi anga ndi kunyazitsidwa kwanga.+
Onse odana nane ali pamaso panu.+
20 Mtima wanga wasweka chifukwa cha chitonzo, ndipo chilonda chake ndi chosachiritsika.+
Ndinali kuyembekezera kuti wina andimvere chifundo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe,+
Ndinali kuyembekezera onditonthoza, koma sanapezeke ngakhale mmodzi.+
21 Koma anandipatsa chomera chakupha kuti ndidye,+
Ndipo anayesa kundimwetsa vinyo wowawasa pamene ndinali ndi ludzu.+
26 Pakuti iwo amalondalonda munthu amene inu mwamulanga,+
Ndipo amakamba za ululu wa anthu amene inu mwawalasa.
31 Zimenezinso zidzasangalatsa kwambiri Yehova kuposa ng’ombe yamphongo,+
Kuposa ng’ombe yamphongo yaing’ono imene ili ndi nyanga, komanso yogawanika ziboda.+
32 Anthu ofatsa adzaona zimenezi ndipo adzakondwera.+
Inu amene mukutumikira Mulungu, mtima wanu ukhalenso ndi moyo.+
34 Kumwamba ndi dziko lapansi zimutamande,+
Chimodzimodzinso nyanja ndi chilichonse choyenda mmenemo.+