17 “Mzimu wanga wasweka,+ masiku anga atha.
Kwanga n’kumanda.+
2 Ndithu, onyoza andizungulira,+
Ndipo diso langa likuyang’anitsitsa khalidwe lawo lopanduka.
3 Chonde, mundisungire chotsimikizira changa.+
Palinso ndani amene angagwirane nane chanza+ monga chikole?
4 Pakuti mtima wawo mwauchititsa kuti ukhale wopanda nzeru.+
N’chifukwa chake simukuwakweza.
5 Munthu angauze anzake kuti atengepo mbali yawo,
Koma maso a ana ake adzachita mdima.+
6 Iye wandisandutsa mwambi+ wa anthu,
Mwakuti ndakhala munthu womulavulira kumaso.+
7 Chifukwa cha kuzunzika, diso langa layamba kuchita mdima.+
Ziwalo zanga zonse zakhala ngati mthunzi.
8 Anthu owongoka mtima akuyang’ana zimenezi modabwa,
Ndipo ngakhale munthu wosalakwa wakwiyira wopanduka.
9 Wolungama akuyendabe panjira yake,+
Ndipo wa manja oyera+ akungowonjezeka mphamvu.+
10 Komabe, amuna nonsenu mungathe kuyambiranso kundinena. Chotero pitirizani,
Chifukwa sindikuonapo wanzeru pakati panu.+
11 Masiku anga atha,+ zolinga zanga zasokonezedwa,+
Zofuna za mtima wanga zasokonezedwa.
12 Anzanga akungokhalira kunena zabodza m’malo monena zoona.+ Iwo akunena kuti:
‘Kuwala kuli pafupi, pamene ine ndikungoona mdima wokhawokha.’
13 Ndikapitiriza kudikira, ku Manda kukhala kunyumba kwanga.+
Ndidzayala bedi langa mu mdima.+
14 Ndidzaitana dzenje+ kuti, ‘Ndinu bambo anga!’
Kwa mphutsi+ ndidzati, ‘Mayi anga ndi mlongo wanga!’
15 Chotero, kodi chiyembekezo changa chili kuti?+
Kodi pali amene akuona kuti ine ndili ndi chiyembekezo?
16 Iwo adzatsikira ku Manda otsekedwa ndi zitsulo,
Pa nthawi imene tonsefe tidzatsikira limodzi kufumbi.”+