115 Ife sitikuyenerera kalikonse, inu Yehova, ife sitikuyenerera kalikonse,+
Koma dzina lanu ndi loyenera kulemekezedwa+
Malinga ndi kukoma mtima kwanu kosatha, malinganso ndi choonadi chanu.+
2 Musalole kuti mitundu izinena kuti:+
“Mulungu wawo ali kuti tsopano?”+
3 Koma Mulungu wathu ali kumwamba.+
Chilichonse chimene anafuna kuchita anachita.+
4 Mafano awo ndi opangidwa ndi siliva ndi golide,+
Ntchito ya manja a munthu wochokera kufumbi.+
5 Pakamwa ali napo koma salankhula,+
Maso ali nawo koma saona.+
6 Makutu ali nawo koma satha kumva.+
Mphuno ali nayo koma sanunkhiza.+
7 Manja ali nawo, koma sakhudza kanthu.+
Mapazi ali nawo koma sayenda.+
Satulutsa mawu ndi mmero wawo.+
8 Amene amawapanga adzafanana nawo.+
Onse amene amawakhulupirira adzakhala ngati mafanowo.+
9 Iwe Isiraeli, khulupirira Yehova.+
Iye ndiye thandizo lako ndi chishango chako.+
10 Inu nyumba ya Aroni, khulupirirani Yehova.+
Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.+
11 Inu oopa Yehova, khulupirirani Yehova.+
Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.+
12 Yehova watikumbukira, ndipo adzapereka madalitso,+
Adzadalitsa nyumba ya Isiraeli,+
Adzadalitsa nyumba ya Aroni.+
13 Yehova adzadalitsa anthu omuopa,+
Adzadalitsa onsewo osasiyapo aliyense.+
14 Yehova adzakuchulukitsani,+
Inu ndi ana anu.+
15 Inu ndinu amene mwadalitsidwa ndi Yehova,+
Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi.+
16 Kunena za kumwamba, kumwamba ndi kwa Yehova,+
Koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.+
17 Akufa satamanda Ya,+
Ngakhalenso aliyense wotsikira kuli chete.+
18 Koma ife tidzatamanda Ya+
Kuyambira tsopano mpaka kalekale.+
Tamandani Ya, anthu inu!+