2 Timoteyo
1 Ine Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu,+ malinga ndi lonjezo la moyo+ loperekedwa kwa ogwirizana ndi Khristu Yesu,+ 2 ndikulembera iwe Timoteyo mwana wanga wokondedwa:+
Kukoma mtima kwakukulu, chifundo, ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu+ zikhale nawe.
3 Ndikuyamika Mulungu, amene ndikumuchitira utumiki wopatulika+ monga mmene makolo anga+ anachitira, ndipo ndikuuchita ndi chikumbumtima choyera.+ Ndikumuyamika chifukwa chakuti sindiiwala za iwe m’mapembedzero anga,+ usana ndi usiku, 4 ndipo ndikakumbukira misozi yako ndimalakalaka kukuona+ kuti ndidzasangalale kwambiri. 5 Pakuti ndikukumbukira chikhulupiriro+ chopanda chinyengo+ chimene uli nacho, chimene chinayamba kukhazikika mwa agogo ako aakazi a Loisi, ndi mayi ako a Yunike, ndipo ndikukhulupirira kuti chilinso mwa iwe.
6 Pa chifukwa chimenechi, ndikukukumbutsa kuti mphatso+ ya Mulungu imene ili mwa iwe, yomwe unailandira pamene ndinaika manja anga pa iwe,+ uikolezere ngati moto.+ 7 Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wamantha,+ koma wamphamvu,+ wachikondi, ndi woti tiziganiza bwino.+ 8 Chotero, usachite manyazi ndi ntchito yochitira umboni za Ambuye wathu,+ kapena za ineyo amene ndine mkaidi chifukwa cha iye.+ Khala wokonzeka kumva zowawa+ mu mphamvu ya Mulungu+ chifukwa cha uthenga wabwino. 9 Iye anatipulumutsa+ ndi kutiitana kuti tikhale oyera,+ osati chifukwa cha ntchito zathu,+ koma mwa chifuniro chake ndi kukoma mtima kwake kwakukulu. Iye anatikomera mtima m’njira imeneyi kalekalelo mwa Khristu Yesu.+ 10 Koma tsopano izi zatsimikizirika bwino chifukwa cha kuonekera+ kwa Mpulumutsi wathu Khristu Yesu, amene wathetsa mphamvu imfa.+ Kudzera mu uthenga wabwino,+ iye watidziwitsa bwinobwino+ mmene tingapezere moyo+ wosawonongeka.+ 11 Uthenga wabwino umenewu ndi umene anandiikira kuti ndikhale mlaliki, mtumwi ndi mphunzitsi.+
12 N’chifukwa chake ndikuvutika chonchi,+ koma sindikuchita manyazi.+ Pakuti ndikudziwa amene ndikumukhulupirira, ndipo ndikukhulupirira kuti adzasunga+ chimene ndachiika m’manja mwake kufikira tsikulo.+ 13 Gwiritsitsabe chitsanzo cha mawu olondola+ amene unawamva kwa ine, komanso chikhulupiriro ndi chikondi zomwe zili mwa Khristu Yesu.+ 14 Chuma chapadera+ chimene anachiika m’manja mwakochi, uchisunge mothandizidwa ndi mzimu woyera umene uli mwa ife.+
15 Iwe ukudziwa kuti anthu onse m’chigawo cha Asia+ andisiya.+ Ena mwa iwo ndi Fugelo ndi Heremogene. 16 Ambuye achitire chifundo banja la Onesiforo,+ chifukwa iye anali kubwera kawirikawiri kudzandilimbikitsa,+ ndipo sanachite manyazi ndi maunyolo anga.+ 17 M’malomwake, pamene anali ku Roma, anandifunafuna mwakhama mpaka anandipeza.+ 18 Ambuye amulole kukapeza chifundo+ chochokera kwa Yehova m’tsikulo.+ Za utumiki wonse umene anachita ku Efeso, iwe ukuzidziwa bwino.