Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 14:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Iwo anafunsa Mose kuti: “Kodi watibweretsa kuno kuti tidzafere mʼchipululu muno chifukwa chakuti mu Iguputo mulibe manda?+ Nʼchifukwa chiyani watichitira zimenezi? Nʼchifukwa chiyani watitulutsa mu Iguputo?

  • Ekisodo 17:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Koma anthuwo anali ndi ludzu kwambiri ndipo anapitiriza kungʼungʼudza motsutsana ndi Mose+ kuti: “Nʼchifukwa chiyani unatitulutsa ku Iguputo kuti udzatiphe ndi ludzu limodzi ndi ana athu ndi ziweto zathu?”

  • Numeri 16:13, 14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Kodi ukuyesa nʼchinthu chachingʼono kuti unatichotsa mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi kuti udzatiphere mʼchipululu muno?+ Kodi tsopano ukufunanso kuti wotilamulira ukhale iwe wekha? 14 Si izi nanga, sunatifikitse kudziko lililonse loyenda mkaka ndi uchi+ kapena kutipatsa malo ndiponso minda ya mpesa. Kodi ukufuna kuti amunawo uwakolowole maso? Tatitu kumeneko sitibwerako!”

  • Numeri 21:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Choncho iwo anayamba kudandaula motsutsana ndi Mulungu komanso Mose+ kuti: “Nʼchifukwa chiyani munatitulutsa mʼdziko la Iguputo kuti tidzafere mʼchipululu muno? Kuno kulibe chakudya komanso madzi,+ ndipo chakudya chonyansachi chafika potikola.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena