3 Chaka chilichonse mwamuna ameneyu ankachoka mumzinda wawo nʼkupita ku Silo, kukalambira Yehova wa magulu ankhondo akumwamba komanso kukapereka nsembe zake.+ Kumeneko nʼkumene ana awiri a Eli, Hofeni ndi Pinihasi,+ ankatumikira monga ansembe a Yehova.+