3 Chaka ndi chaka mwamuna ameneyu anali kutuluka mumzinda wake n’kupita ku Silo,+ kukagwada ndi kuweramira pansi+ pamaso pa Yehova wa makamu ndi kupereka nsembe zake. Kumeneko n’kumene ana awiri a Eli, Hofeni ndi Pinihasi,+ anali kutumikira monga ansembe a Yehova.+