-
2 Mafumu 22:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Mfumu ya Yuda imene yakutumani kuti mudzafunse kwa Yehova, mukaiuze kuti, “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: ‘Ponena za mawu amene wamvawo, 19 chifukwa chakuti mtima wako unali womvera* ndipo unadzichepetsa+ pamaso pa Yehova utamva zimene ndanena zokhudza malo ano ndi anthu ake, kuti malowa adzakhala chinthu chodabwitsa ndi temberero ndipo unangʼamba zovala zako+ nʼkuyamba kulira pamaso panga, ineyo ndamva, watero Yehova.
-
-
Luka 15:22-24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Koma bambowo anauza akapolo ake kuti, ‘Fulumirani, tengani mkanjo wabwino kwambiri uja mumuveke. Mumuvekenso mphete kudzanja lake ndi nsapato kumapazi kwake. 23 Komanso mubweretse mwana wa ngʼombe wamphongo wonenepa, mumuphe ndipo tidye ndi kusangalala. 24 Chifukwa mwana wangayu anali wakufa koma tsopano wakhalanso ndi moyo,+ anatayika koma wapezeka.’ Choncho onse anayamba kusangalala.
-
-
Luka 18:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Koma wokhometsa msonkho uja, ataima chapatali ndithu, sanafune ngakhale kukweza maso ake kumwamba. Iye ankangodziguguda pachifuwa nʼkumanena kuti, ‘Mulungu wanga, ndikomereni mtima* munthu wochimwa ine.’+ 14 Ndithu ndikukuuzani, munthu ameneyu anapita kwawo ataonedwa kuti ndi wolungama kwambiri kuposa Mfarisi uja.+ Chifukwa aliyense wodzikweza adzachititsidwa manyazi, koma aliyense amene amadzichepetsa adzakwezedwa.”+
-