-
1 Samueli 26:8-10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Ndiyeno Abisai anauza Davide kuti: “Lero Mulungu wapereka mdani wanu mʼmanja mwanu.+ Bwanji ndimubaye ndi mkondo nʼkumukhomerera pansi? Ndimubaya kamodzi kokha, sindichita kubwereza kawiri.” 9 Koma Davide anauza Abisai kuti: “Ayi, usamubaye. Ndani angavulaze wodzozedwa wa Yehova+ nʼkukhala wopanda mlandu?”+ 10 Davide anapitiriza kuti: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova, Mulungu wamoyo, Yehova adzamulanga yekha,+ kapena tsiku lidzafika+ ndipo adzamwalira, kapenanso adzapita kunkhondo nʼkukaphedwa.+
-
-
Salimo 37:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
Usakhumudwe ndi munthu
Amene amakonza ziwembu nʼkuzikwaniritsa popanda vuto lililonse.+
-