-
Danieli 3:26, 27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Nebukadinezara anayandikira khomo la ngʼanjo yoyaka motoyo nʼkunena kuti: “Shadireki, Misheki ndi Abedinego, inu atumiki a Mulungu Wamʼmwambamwamba,+ tulukani ndipo mubwere kuno!” Atatero, Shadireki, Misheki ndi Abedinego anatuluka pakati pa motowo. 27 Masatarapi, akuluakulu a boma, abwanamkubwa ndi nduna zapamwamba za mfumu amene anasonkhana kumeneko,+ anaona kuti amuna amenewa+ motowo sunawawotche* ngakhale pangʼono. Tsitsi la kumutu kwawo ndi limodzi lomwe silinawauke. Zovala zawo sizinasinthe ndipo sankamveka ngakhale fungo la moto.
-