Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Danieli 2:44
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 44 Mʼmasiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu+ umene sudzawonongedwa.+ Ufumu umenewu sudzaperekedwa kwa anthu a mtundu wina uliwonse.+ Koma udzaphwanya nʼkuthetsa maufumu ena onsewa+ ndipo ndi ufumu wokhawu umene udzakhalepo mpaka kalekale.+

  • Danieli 7:13, 14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Ndinapitiriza kuona masomphenya usikuwo ndipo ndinaona winawake wooneka ngati mwana wa munthu+ akubwera mʼmitambo. Iye analoledwa kufika kwa Wamasiku Ambiri+ uja ndipo anamubweretsa pafupi kwambiri ndi Wamasiku Ambiriyo. 14 Kenako anamupatsa ulamuliro,+ ulemu+ ndi ufumu kuti anthu a mitundu yonse komanso anthu olankhula zilankhulo zosiyanasiyana azimutumikira.+ Ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.+

  • Mateyu 6:9-13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Koma inu muzipemphera chonchi:+

      ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu+ liyeretsedwe.*+ 10 Ufumu wanu ubwere.+ Zofuna zanu+ zichitike padziko lapansi pano ngati mmene zilili kumwamba.+ 11 Mutipatse chakudya chimene* tikufunikira lero.+ 12 Mutikhululukire zolakwa* zathu chifukwa ifenso takhululukira amene atilakwira.*+ 13 Tithandizeni kuti tisagonje tikamayesedwa,*+ koma mutiteteze kwa woipayo.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena