19 Koma akadzakupititsani kumeneko, musadzade nkhawa kuti mudzalankhula bwanji kapena kuti mudzanena chiyani, chifukwa zoti mulankhule mudzapatsidwa nthawi yomweyo.+ 20 Zili choncho chifukwa wolankhula simudzakhala inu nokha, koma mzimu wa Atate wanu udzalankhula kudzera mwa inu.+